Mavesi a m'Baibulo Onena za Chipulumutso
Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Chipulumutso oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
kuti ngati udzavomereza ndi pakamwa pako kuti, “Yesu ndiye Ambuye,” ndi kukhulupirira mu mtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.
Chipulumutso sichipezeka mwa wina aliyense; pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo limene lapatsidwa kwa anthu limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.”
Pakuti ndi mtima wanu mukhulupirira ndi kulungamitsidwa, ndipo ndi pakamwa panu muvomereza ndi kupulumutsidwa.
Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake ku dziko lapansi, kuti akaweruze, koma kuti akapulumutse dziko lapansi.
Pakuti chisomo cha Mulungu chimene chimapulumutsa chaonekera kwa anthu onse.
Pakuti akunena kuti, “Pa nthawi yanga yabwino yokomera anthu mtima ndinakumvera, ndipo pa nthawi yopulumutsa ndinakuthandiza. Taonani, ndikukuwuzani kuti, ino ndiyo nthawi yabwino ya Ambuye, lero ndiye tsiku la chipulumutso.”
amene amafuna kuti anthu onse apulumutsidwe ndipo kuti adziwe choonadi.