Mavesi a m'Baibulo Onena za Khomo Lopapatiza

Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Khomo Lopapatiza oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Mateyu 7:13-14

“Lowani pa chipata chopapatiza. Pakuti chipata cholowera kuchiwonongeko nʼchachikulu ndipo msewu wake ndi waukulunso. Ndipo anthu ambiri amalowera pamenepo. Koma chipata ndi chopapatiza ndi msewu ndi waungʼono umene utsogolera anthu ku moyo wosatha ndipo ndi owerengeka okha amene ayipeza njirayo.

02 Luka 13:24

“Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza, chifukwa ndikukuwuzani kuti ambiri adzafuna kulowa koma sadzatha kutero.

03 Yohane 14:6

Yesu anayankha kuti, “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate popanda kudzera mwa Ine.

04 Mateyu 7:21

“Si munthu aliyense amene amanena kwa Ine, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowe mu ufumu wakumwamba, koma ndi yekhayo amene amachita chifuniro cha Atate anga amene ali kumwamba.

05 Miyambo 14:12

Pali njira ina yooneka ngati yabwino kwa munthu, koma kumatsiriziro kwake ndi ku imfa.

06 Luka 13:23-24

Wina anamufunsa Iye kuti, “Ambuye, kodi ndi anthu ochepa okha amene adzapulumutsidwe?” Iye anawawuza kuti, “Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza, chifukwa ndikukuwuzani kuti ambiri adzafuna kulowa koma sadzatha kutero.

07 Yohane 10:9

Ine ndine khomo, aliyense amene alowa kudzera mwa Ine adzapulumuka. Iye adzalowa ndi kutuluka ndi kupeza msipu.

Chipulumutso sichipezeka mwa wina aliyense; pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo limene lapatsidwa kwa anthu limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.”

09 Mateyu 16:24

Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Ngati wina aliyense abwera pambuyo panga ayenera kudzikana ndi kutenga mtanda wake ndi kunditsata Ine.

10 Luka 9:23

Ndipo Iye anawuza onse kuti, “Ngati wina aliyense akufuna kutsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kusenza mtanda wake tsiku ndi tsiku nʼkumanditsata Ine.

11 Mateyu 7:22-23

Ambiri adzati kwa Ine pa tsikulo, ‘Ambuye, Ambuye, kodi sitinkanenera mʼdzina lanu ndi mʼdzina lanunso tinkatulutsa ziwanda ndi kuchita zodabwitsa zambiri?’ Pamenepo ndidzawawuza momveka bwino kuti, ‘Sindinakudziweni inu. Chokani kwa Ine, inu ochita zoyipa!’

12 Ahebri 12:14

Yesetsani kukhala pa mtendere ndi anthu onse ndi kukhala oyera mtima, pakuti popanda chiyero palibe ndi mmodzi yemwe adzaona Ambuye.

13 2 Petro 1:10

Nʼchifukwa chake abale anga, funitsitsani kuti mayitanidwe ndi masankhidwe anu akhale otsimikizika. Pakuti ngati muchita zinthu izi, simudzagwa konse.

14 Yohane 10:7

Choncho Yesu anatinso, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Ine ndine khomo la nkhosa.

Mitu yofanana