Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuchoka ku Imfa Kupita ku Moyo
Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Kuchoka ku Imfa Kupita ku Moyo oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
“Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene amamva mawu anga ndi kukhulupirira Iye amene ananditumiza Ine, ali ndi moyo wosatha ndipo sadzaweruzidwa. Iye wachoka mu imfa ndipo walowa mʼmoyo.
Koma chifukwa cha chikondi chake chachikulu pa ife, Mulungu amene ndi olemera mʼchifundo, anatipanga kukhala amoyo ndi Khristu ngakhale pamene ife tinali akufa mu zolakwa zathu. Koma tinapulumutsidwa mwachisomo.
Pamene munali akufa chifukwa cha machimo anu ndi osachita mdulidwe mʼmitima mwanu, Mulungu anakupatsani moyo mwa Khristu. Iye anatikhululukira machimo athu onse.
Ife tikudziwa kuti tinatuluka mu imfa ndi kulowa mʼmoyo, chifukwa timakonda abale athu. Aliyense amene sakonda mʼbale wake akanali mu imfa.
Musapereke ziwalo zathupi lanu ku tchimo, ngati zipangizo zamakhalidwe oyipa. Mʼmalo mwake, mudzipereke kwa Mulungu, ngati amene achoka ku imfa kupita ku moyo. Ndipo mupereke ziwalo zathupi lanu ngati zipangizo zachilungamo.
Yesu anati kwa iye, “Ine ndine kuuka ndi moyo. Wokhulupirira Ine, angakhale amwalira adzakhala ndi moyo. Aliyense amene ali ndi moyo ndi kukhulupirira Ine sadzamwalira. Kodi iwe ukukhulupirira izi?”
Chifukwa chake ife tinayikidwa mʼmanda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo. Tinalowa mu imfa ndi cholinga choti monga momwe Khristu anaukitsidwa kwa akufa ndi ulemerero wa Atate, ifenso tikakhale mʼmoyo watsopano.
Ndinapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano mʼthupi lino, ndi moyo mwachikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu, amene anandikonda nadzipereka yekha chifukwa cha ine.
Iye mwini anasenza machimo athu mʼthupi lake pa mtanda, kuti ife tife kutchimo ndi kukhala ndi moyo potsata chilungamo, ndipo ndi mabala ake munachiritsidwa.
Kunena za inu, kale munali akufa chifukwa cha zolakwa zanu ndi machimo anu,
Ndipo ngati Mzimu wa Mulungu amene anaukitsa Yesu kwa akufa akhala mwa inu, Iyeyo amene anaukitsa Khristu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu amene amafa kudzera mwa Mzimu wake amene amakhala mwa inu.