Mavesi a m'Baibulo Onena za Moyo Wosatha

Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Moyo Wosatha oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Yohane 3:16

“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha.

02 Yohane 10:28

Ine ndimazipatsa moyo wosatha ndipo sizidzawonongeka. Palibe amene adzazikwatula mʼdzanja langa.

03 Yohane 17:3

Tsono moyo wosathawo ndi uwu: Iwo akudziweni Inu, Mulungu yekhayo woona, ndi Yesu Khristu, amene Inu mwamutuma.

04 1 Yohane 5:11-12

Ndipo umboniwo ndi uwu: Mulungu anatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowu uli mwa Mwana wake. Iye amene ali ndi Mwana ali ndi moyo, amene alibe Mwana wa Mulungu alibe moyo.

05 Yohane 6:47

Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Iye amene akhulupirira ali nawo moyo wosatha.

06 Aroma 6:23

Pakuti malipiro a tchimo ndi imfa, koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

07 1 Yohane 5:13

Ine ndikulemba zimenezi kwa inu, amene mwakhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha.

08 Tito 1:2

ndi kuwapatsa chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu amene sanama, analonjeza nthawi isanayambe.

Mitu yofanana