Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuwomboledwa
Mavesi 13 a m'Baibulo onena za Kuwomboledwa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Mwa Yesu Khristu, chifukwa cha magazi ake, ife tinawomboledwa ndi kukhululukidwa machimo athu molingana ndi kuchuluka kwa chisomo cha Mulungu
Pakuti Iye anatipulumutsa ku ulamuliro wa mdima ndi kutibweretsa mu ufumu wa Mwana wake wokondedwa. Mwa Iyeyu ife tinawomboledwa ndi kukhululukidwa machimo.
amene anadzipereka yekha chifukwa cha ife kutiwombola ku zoyipa zonse ndi kudziyeretsera yekha anthu amene ndi akeake, achangu pa ntchito yabwino.
Pakuti mukudziwa kuti simunawomboledwe ndi zinthu zimene zimawonongeka monga siliva kapena golide, kuchoka ku khalidwe lanu lachabe limene munalandira kwa makolo anu. Koma munawomboledwa ndi magazi a mtengowapatali a Khristu, Mwana Wankhosa wopanda banga kapena chilema.
Khristu anatiwombola ku temberero la lamulo pokhala temberero mʼmalo mwathu, pakuti analemba kuti, “Aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa.”
ndipo onse alungamitsidwa mwaulere mwa chisomo chake chifukwa cha Khristu Yesu amene anawawombola.
Ndinu ochita kugulidwa. Nʼchifukwa chake lemekezani Mulungu mʼthupi lanu.
Iye sanalowemo ndi magazi ambuzi yayimuna, ana angʼombe amphongo, koma analowa Malo Opatulika kamodzi kokha ndi magazi ake, atatikonzera chipulumutso chosatha.
Si zokhazo ayi, ngakhale ife tomwe, amene tili ndi zipatso zoyamba za Mzimu, tikubuwulira mʼkati mwathu pomwe tikudikira mwachidwi kusankhidwa kwathu ngati ana, kuwomboledwa kwa matupi athu.
“Alemekezeke Ambuye, Mulungu wa Israeli chifukwa wabwera ndi kuwombola anthu ake.
Ndipo ankayimba nyimbo yatsopano yakuti, “Inu ndinu woyenera kulandira bukuli ndi kumatula zomatira zake, chifukwa munaphedwa, ndipo magazi anu munagulira Mulungu anthu a fuko lililonse, a chiyankhulo chilichonse, ndi mtundu uliwonse.
Yembekeza Yehova, iwe Israeli, pakuti Yehova ali ndi chikondi chosasinthika ndipo alinso ndi chipulumutso chochuluka.
Nʼchifukwa cha Iye kuti inu muli mwa Khristu Yesu, amene wakhala nzeru ya kwa Mulungu, kwa ife, kunena kuti kulungama kwathu, chiyero ndi chipulumutso.