Mavesi a m'Baibulo Onena za Mtumiki Wovutika
Mavesi 10 a m'Baibulo onena za Mtumiki Wovutika oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu, munthu amene moyo wake unali wamasautso, wozolowera zowawa, ndipo anali ngati munthu amene anzake amaphimba nkhope zawo akamuona. Iye ananyozedwa, ndipo ife sitinamuyese kanthu.
Koma iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, ndipo anamuzunza chifukwa cha zoyipa zathu; iye analangidwa kuti ife tikhale ndi mtendere, ndipo ndi mabala ake ife tinachiritsidwa.
Anthu anamuzunza ndi kumusautsa, koma sanayankhule kanthu. Monga mwana wankhosa wopita naye kokamupha amachitira, kapena monga nkhosa imakhalira duu poyimeta, momwemonso iye sanatsekule pakamwa pake.
Anthu ambiri atamuona anadzidzimuka, chifukwa nkhope yake inali itasakazika; sinalinso ngati ya munthu. Ndipo thupi lake linasakazika; silinalinso ngati la munthu.
Koma anadzichepetsa kotheratu nakhala ndi khalidwe ngati la kapolo ndi kukhala munthu ngati anthu ena onse. Ndipo pokhala munthu choncho anadzichepetsa yekha ndipo anamvera mpaka imfa yake, imfa yake ya pamtanda!
Ndithudi, iye anamva zowawa mʼmalo mwa ife; ndipo anasautsidwa mʼmalo mwathu. Koma ife tinkaganiza kuti ndi Mulungu amene akumulanga, kumukantha ndi kumusautsa.
Ife tonse, ngati nkhosa, tasochera, aliyense mwa ife akungodziyendera; ndipo Yehova wamusenzetsa zoyipa zathu zonse.
Komatu ndi Yehova amene anafuna kuti amuzunze ndi kumusautsa. Yehova anapereka moyo wa mtumiki wake kuti ukhale nsembe yoperekedwa chifukwa cha zolakwa. Tsono iye adzaona zidzukulu zake ndipo adzakhala ndi moyo wautali, ndipo chifuniro cha Yehova chidzachitika mwa iye.
Ndinapereka msana wanga kwa ondimenya masaya anga ndinawapereka kwa anthu ondizula ndevu; sindinawabisire nkhope yanga anthu ondinyoza ndi ondilavulira.
Atatha mazunzo a moyo wake, adzaona kuwala, ndipo adzakhutira. Mwa nzeru zake mtumiki wanga wolungamayo adzalungamitsa anthu ambiri, popeza adzasenza zolakwa zawo.