Mavesi a m'Baibulo Onena za Mwanawankhosa wa Mulungu

Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Mwanawankhosa wa Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Yohane 1:29

Pa tsiku lotsatira Yohane anaona Yesu akubwera kwa iye ndipo anati, “Taonani, Mwana Wankhosa wa Mulungu, amene achotsa tchimo la dziko lapansi!

02 Yesaya 53:7

Anthu anamuzunza ndi kumusautsa, koma sanayankhule kanthu. Monga mwana wankhosa wopita naye kokamupha amachitira, kapena monga nkhosa imakhalira duu poyimeta, momwemonso iye sanatsekule pakamwa pake.

03 Chivumbulutso 5:12

Ndipo angelowo anayimba ndi mawu ofuwula akuti, “Mwana Wankhosa amene anaphedwayu ndi woyenera kulandira ulamuliro, chuma, nzeru, mphamvu, ulemu, ulemerero ndi mayamiko.”

04 1 Petro 1:19

Koma munawomboledwa ndi magazi a mtengowapatali a Khristu, Mwana Wankhosa wopanda banga kapena chilema.

05 Chivumbulutso 5:6

Kenaka ndinaona Mwana Wankhosa akuoneka ngati wophedwa atayimirira pakatikati pa mpando waufumu uja ndi zamoyo zinayi zija ndi akuluakulu aja. Mwana Wankhosayo anali ndi nyanga zisanu ndi ziwiri ndi maso asanu ndi awiri omwe ndi Mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu yomwe anayitumiza ku dziko lonse lapansi.

06 Yohane 1:36

Iye ataona Yesu akudutsa anati, “Taonani Mwana Wankhosa wa Mulungu!”

07 1 Akorinto 5:7

Chotsani yisiti wakale kuti mukhale ndi mphumphu yopanda yisiti, monga inu muli. Pakuti Khristu, Mwana Wankhosa wa Paska wathu, anaperekedwa nsembe.

08 Chivumbulutso 5:9

Ndipo ankayimba nyimbo yatsopano yakuti, “Inu ndinu woyenera kulandira bukuli ndi kumatula zomatira zake, chifukwa munaphedwa, ndipo magazi anu munagulira Mulungu anthu a fuko lililonse, a chiyankhulo chilichonse, ndi mtundu uliwonse.

09 Chivumbulutso 7:14

Ine ndinayankha kuti, “Mbuye wanga mukudziwa ndinu.” Tsono iye anandiwuza kuti, “Amenewa ndi amene anatuluka mʼmazunzo aakulu aja. Anachapa mikanjo yawo naziyeretsa mʼmagazi a Mwana Wankhosa.

Abale athuwo anamugonjetsa ndi magazi a Mwana Wankhosa ndiponso mawu a umboni wawo. Iwo anadzipereka kwathunthu, moti sanakonde miyoyo yawo.

Mawu amene ndunayo imawerenga anali awa: “Monga mwana wankhosa wopita naye kokamupha amachitira, kapena monga nkhosa imakhalira duu poyimeta, momwemonso iye sanatsekule pakamwa pake.

Mitu yofanana