Mavesi a m'Baibulo Onena za Anasenza Machimo Athu

Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Anasenza Machimo Athu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Yesaya 53:5

Koma iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, ndipo anamuzunza chifukwa cha zoyipa zathu; iye analangidwa kuti ife tikhale ndi mtendere, ndipo ndi mabala ake ife tinachiritsidwa.

02 1 Petro 2:24

Iye mwini anasenza machimo athu mʼthupi lake pa mtanda, kuti ife tife kutchimo ndi kukhala ndi moyo potsata chilungamo, ndipo ndi mabala ake munachiritsidwa.

03 Yesaya 53:6

Ife tonse, ngati nkhosa, tasochera, aliyense mwa ife akungodziyendera; ndipo Yehova wamusenzetsa zoyipa zathu zonse.

04 2 Akorinto 5:21

Chifukwa cha ife, Mulungu anasandutsa wopanda tchimoyo kukhala tchimo, kuti mwa Iye ife tikakhale chilungamo cha Mulungu.

05 Yesaya 53:11

Atatha mazunzo a moyo wake, adzaona kuwala, ndipo adzakhutira. Mwa nzeru zake mtumiki wanga wolungamayo adzalungamitsa anthu ambiri, popeza adzasenza zolakwa zawo.

06 Yesaya 53:4

Ndithudi, iye anamva zowawa mʼmalo mwa ife; ndipo anasautsidwa mʼmalo mwathu. Koma ife tinkaganiza kuti ndi Mulungu amene akumulanga, kumukantha ndi kumusautsa.

07 Yesaya 53:12

Motero Ine ndidzamupatsa ulemu pamodzi ndi akuluakulu, adzagawana zofunkha ndi ankhondo amphamvu, popeza anapereka moyo wake mpaka kufa, ndipo anamuyika mʼgulu la anthu olakwa kuti akhululukidwe. Pakuti iye anasenza machimo a anthu ambiri, ndipo anawapempherera anthu olakwa.

08 Ahebri 9:28

momwemonso Khristu anadzipereka nsembe kamodzi kokha kuchotsa machimo a anthu ambiri. Ndipo Iye adzaonekanso kachiwiri, osati kudzachotsa tchimo, koma kudzapereka chipulumutso kwa amene akumudikira.

09 1 Petro 3:18

Pakuti Khristu anafa chifukwa cha machimo kamodzi kokha kufera onse, wolungama kufera osalungama, kuti akufikitseni kwa Mulungu. Anaphedwa ku thupi koma anapatsidwa moyo mu mzimu.

10 Agalatiya 1:4

Yesuyo anadzipereka yekha chifukwa cha machimo athu kuti atipulumutse ku njira za moyo woyipa uno, molingana ndi chifuniro cha Mulungu ndi Atate athu.

11 Yohane 1:29

Pa tsiku lotsatira Yohane anaona Yesu akubwera kwa iye ndipo anati, “Taonani, Mwana Wankhosa wa Mulungu, amene achotsa tchimo la dziko lapansi!

Mitu yofanana