Mavesi a m'Baibulo Onena za Magazi a Khristu

Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Magazi a Khristu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 1 Petro 1:18-19

Pakuti mukudziwa kuti simunawomboledwe ndi zinthu zimene zimawonongeka monga siliva kapena golide, kuchoka ku khalidwe lanu lachabe limene munalandira kwa makolo anu. Koma munawomboledwa ndi magazi a mtengowapatali a Khristu, Mwana Wankhosa wopanda banga kapena chilema.

02 Aefeso 1:7

Mwa Yesu Khristu, chifukwa cha magazi ake, ife tinawomboledwa ndi kukhululukidwa machimo athu molingana ndi kuchuluka kwa chisomo cha Mulungu

03 Ahebri 9:22

Monga mwa malamulo titha kunena kuti, pafupifupi zinthu zonse zimayeretsedwa ndi magazi ndipo popanda kukhetsa magazi palibe kukhululukidwa machimo.

04 Chivumbulutso 1:5

ndiponso kuchokera kwa Yesu Khristu mboni yokhulupirika, woyamba kuukitsidwa, ndi wolamulira mafumu a dziko lapansi. Kwa Iye amene amatikonda ndipo watimasula ku machimo athu ndi magazi ake,

05 Aroma 5:9

Popeza chifukwa cha magazi ake ife tapezeka olungama pamaso pa Mulungu, Iyeyo adzatipulumutsa koposa kotani ku mkwiyo wa Mulungu.

06 Ahebri 9:14

nʼkoposa kotani magazi a Khristu, amene mwa Mzimu wamuyaya anadzipereka yekha kwa Mulungu kukhala nsembe yopanda chilema. Iye adzayeretsa chikumbumtima chathu pochotsa ntchito za imfa, kuti ife titumikire Mulungu wamoyo.

07 Ahebri 13:12

Nʼchifukwa chakenso Yesu anafera kunja kwa mzinda kuti ayeretse anthu ake kudzera mʼmagazi ake.

08 1 Yohane 1:7

Koma tikamayenda mʼkuwunika, monga Iye ali mʼkuwunika, pamenepo timayanjana wina ndi mnzake, ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.

Mitu yofanana