Mavesi a m'Baibulo Onena za Kwatha
Mavesi 13 a m'Baibulo onena za Kwatha oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Yesu atalandira chakumwachi anati, “Kwatha.” Ndipo Iye anaweramitsa mutu wake napereka mzimu wake.
Koma pamene wansembe uyu anapereka kamodzi kokha nsembe imodzi yokha chifukwa cha machimo, Iye anakhala pansi ku dzanja lamanja la Mulungu.
Iye sanalowemo ndi magazi ambuzi yayimuna, ana angʼombe amphongo, koma analowa Malo Opatulika kamodzi kokha ndi magazi ake, atatikonzera chipulumutso chosatha.
Anafafaniza kalata ya ngongole yathu, pomwe panali milandu yotitsutsa ife. Iye anayichotsa, nayikhomera pa mtanda.
Choncho, tsopano amene ali mwa Khristu Yesu alibe mlandu owatsutsa
Chifukwa cha nsembe imodzi Iye anasandutsa angwiro kwamuyaya iwo amene akuwayeretsa.
Ine ndabweretsa ulemerero wanu pa dziko pamene ndamaliza ntchito imene munandipatsa kuti ndi igwire.
Mwanayo ndiye kuwala kwa ulemerero wa Mulungu, chithunzithunzi chenicheni cha khalidwe lake. Iyeyu amachirikiza zinthu zonse ndi mphamvu ya mawu ake. Iye atayeretsa anthu kuchoka ku machimo awo, anakhala pansi kumwamba kudzanja lamanja la Mulungu waulemerero.
Kusiyana ndi akulu a ansembe ena aja, Yesu sanafunike kupereka nsembe tsiku ndi tsiku poyamba chifukwa cha machimo ake, ndipo kenaka chifukwa cha machimo a anthu ena. Iye anadzipereka nsembe chifukwa cha machimo awo kamodzi kokha pamene anadzipereka yekha.
Imfa imene Iye anafa, anafa ku tchimo kamodzi kokha, koma moyo umene akhala ndi wa kwa Mulungu.
Zikanatero bwenzi Khristu atamva zowawa kambirimbiri chilengedwere cha dziko lapansi. Koma tsopano anaoneka kamodzi kokha chifukwa cha onse pa nthawi yotsiriza kuti achotse tchimo podzipereka yekha nsembe.
Atadziwa kuti zonse zatha tsopano komanso kuti malemba akwaniritsidwe, Yesu anati, “Ine ndili ndi ludzu.”
Pakuti Khristu anafa chifukwa cha machimo kamodzi kokha kufera onse, wolungama kufera osalungama, kuti akufikitseni kwa Mulungu. Anaphedwa ku thupi koma anapatsidwa moyo mu mzimu.