Mavesi a m'Baibulo Onena za Mutamandeni Kumwambamwamba
Mavesi 13 a m'Baibulo onena za Mutamandeni Kumwambamwamba oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Tamandani Yehova. Tamandani Yehova, inu a kumwamba, mutamandeni Iye, inu a mlengalenga.
Mutamandeni, inu angelo ake onse, mutamandeni, mutamandeni, inu zolengedwa za mmwamba. Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi, mutamandeni, inu nonse nyenyezi zowala.
Onsewo atamande dzina la Yehova pakuti dzina lake lokha ndi lolemekezeka; ulemerero wake ndi woopsa pa dziko lapansi pano ndi kumwamba komwe.
Zakumwamba zimalengeza za ulemerero wa Mulungu; thambo limalalikira ntchito za manja ake.
Tamandani Yehova. Tamandani Mulungu mʼmalo ake opatulika; mutamandeni ku thambo lake lamphamvu.
Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Yehova. Tamandani Yehova.
Mayiko akumwamba amatamanda zozizwitsa zanu Yehova, kukhulupirika kwanunso, mu msonkhano wa oyera mtima anu.
Ndipo Aserafiwo amafuwulirana kuti “Woyera, woyera, woyera Yehova Wamphamvuzonse. Dziko lonse lapansi ladzaza ndi ulemerero wake.”
Chamoyo chilichonse chinali ndi mapiko asanu ndi limodzi, ndipo chinali ndi maso ponseponse ndi mʼkati mwa mapiko momwe. Usana ndi usiku zimanena mosalekeza kuti, “Woyera, woyera, woyera ndi Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse, amene munali, amene muli ndi amene mukubwera.”
Mayiko akumwamba asangalale, dziko lapansi likondwere; nyanja ikokome, ndi zonse zili mʼmenemo;
Mutamandeni, inu thambo la kumwambamwamba ndi inu madzi a pamwamba pa thambo.
Inu nokha ndiye Yehova. Munalenga kumwamba, ngakhale kumwambamwamba, zolengedwa zonse zimene zili mʼmenemo. Munalenga dziko ndi zonse zokhalamo, nyanja ndi zonse zili mʼmenemo. Zonse mumazisunga ndi moyo ndipo zonse za kumwamba zimakupembedzani.
Tamandani Yehova, inu angelo ake, amphamvu inu amene mumachita zimene amalamula, amene mumamvera mawu ake. Tamandani Yehova, zolengedwa zonse zakumwamba, inu atumiki ake amene mumachita chifuniro chake.