Mavesi a m'Baibulo Onena za Thupi Limodzi

Mavesi 13 a m'Baibulo onena za Thupi Limodzi oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Marko 10:8

ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.’ Potero sali awirinso, koma mmodzi.

02 Genesis 2:24

Nʼchifukwa chake, mwamuna amasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake ndipo awiriwo amakhala thupi limodzi.

03 Aefeso 5:31

“Pa chifukwa ichi, mwamuna adzasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.”

04 Marko 10:9

Chifukwa chake chimene Mulungu wachilumikiza pamodzi, munthu wina asachilekanitse.”

05 1 Akorinto 6:16

Kodi simukudziwa kuti amene amadzipereka kwa mkazi wadama, iyeyo ndi mkaziyo amasanduka thupi limodzi? Paja kunalembedwa kuti, “Awiriwo adzakhala thupi limodzi.”

06 Genesis 2:23

Munthu uja anati, “Uyu ndiye fupa lochokera ku mafupa anga ndi mnofu wochokera ku mnofu wanga; adzatchedwa ‘mkazi,’ popeza wachokera mwa mwamuna.”

07 Mateyu 19:5-6

Ndipo anati, ‘Pa chifukwa ichi mwamuna adzasiya abambo ake ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.’ Motero salinso awiri ayi koma mmodzi. Nʼchifukwa chake chimene Mulungu wachimanga pamodzi munthu wina asachilekanitse.”

08 Aefeso 5:28-31

Momwemonso, amuna akuyenera kukonda akazi awo monga matupi awo. Iye amene akonda mkazi wake adzikondanso yekha. Pakuti palibe amene amadana nalo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulisamalira bwino, monga momwe Khristu amachitira ndi mpingo wake pakuti ndife ziwalo za thupi lake. “Pa chifukwa ichi, mwamuna adzasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.”

09 Genesis 2:25

Munthu uja ndi mkazi wakeyo, onse awiri anali maliseche ndipo analibe manyazi.

10 1 Akorinto 7:4

Thupi la mkazi wokwatiwa si la iye mwini yekha koma ndi la mwamuna wakenso. Momwemonso, thupi la mwamuna si la iye mwini yekha koma ndi la mkazi wakenso.

11 Malaki 2:15

Kodi Yehova sanawalenge iwo ngati munthu mmodzi? Ndi ake mʼthupi ndi mu mzimu. Nʼchifukwa chiyani ali mmodzi? Chifukwa Iye amafuna ana opembedza Mulungu. Motero samala moyo wako wauzimu, ndipo usakhale wosakhulupirika kwa mkazi wa unyamata wako.

12 Miyambo 18:22

Wapeza mkazi wapeza chinthu chabwino ndipo Yehova amamukomera mtima.

13 Aroma 7:2

Mwachitsanzo, Malamulo amati mkazi wokwatiwa ndi womangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wakeyo nthawi yonse pamene mwamuna wakeyo ali moyo. Koma ngati mwamuna wake amwalira, mkaziyo ndi womasulidwa ku lamulo la ukwati.

Mitu yofanana