Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuwala kwa Mitundu ya Anthu

Mavesi 10 a m'Baibulo onena za Kuwala kwa Mitundu ya Anthu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Yesaya 49:6

Yehovayo tsono akuti, “Nʼchinthu chochepa kwambiri kwa iwe kuti ukhale mtumiki wanga, kuti udzutse mafuko a Yakobo ndi kuwabweretsa kwawo Aisraeli amene anapulumuka. Choncho iwe udzakhala ngati chowunikira, udzafikitsa uthenga wa chipulumutso changa ku mathero a dziko lapansi.”

02 Mateyu 5:14

“Inu ndinu kuwunika kwa dziko lapansi. Mzinda wa pa phiri sungathe kubisika.

Pakuti izi ndi zimene Ambuye anatilamula ife: “ ‘Ine ndakuyika iwe ukhale kuwunika kwa anthu a mitundu ina, kuti ukafikitse chipulumutso ku malekezero a dziko lapansi!’ ”

04 Yesaya 42:6

“Ine Yehova, ndakuyitana chifukwa Ine ndine wolungama; ndikugwira dzanja ndipo ndidzakuteteza. Ndakupereka kukhala pangano langa kwa anthu ndi kuwunika kwa anthu a mitundu ina.

05 Yohane 8:12

Yesu atayankhulanso kwa anthu, anati, “Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi. Aliyense amene anditsata Ine sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuwala kotsogolera anthu ku moyo.”

06 Mateyu 5:16

Momwemonso kuwunika kwanu kuwale pamaso pa anthu kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kulemekeza Atate anu akumwamba.

07 Afilipi 2:15

kuti mukhale wopanda cholakwa ndi angwiro, ana a Mulungu wopanda cholakwika mu mʼbado uno wachinyengo ndi wosocheretsa. Mukatero mudzawala pakati pawo ngati nyenyezi zakumwamba

kuti ukatsekule maso awo kuti atembenuke mtima kuchoka ku mdima ndi kulowa mʼkuwala, kuchoka ku mphamvu za Satana ndi kupita kwa Mulungu, kuti alandire chikhululukiro cha machimo awo ndi kukhala mʼgulu la amene akuyeretsedwa chifukwa chokhulupirira Ine.

09 Yesaya 60:1-3

“Dzuka, wala, pakuti kuwala kwako kwafika, ndipo ulemerero wa Yehova wakuwalira. Taona, mdima waphimba dziko lapansi ndipo mdima wandiweyani wagwa pa anthu a mitundu ina, koma Yehova adzakuwalira iwe, ndipo ulemerero wake udzaoneka pa iwe. Mitundu ya anthu idzatsata kuwunika kwako ndipo mafumu adzalondola kunyezimira kwa mʼbandakucha wako.

10 1 Petro 2:9

Koma inu ndinu anthu osankhidwa ndi Mulungu, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu ake enieni a Mulungu, munasankhidwa kuti mulalikire za ntchito zamphamvu za Iye amene anakuyitanani kuti mutuluke mu mdima ndi kulowa mʼkuwunika kwake kodabwitsa.

Mitu yofanana