Mavesi a m'Baibulo Onena za Akukhalabe Wamoyo Kuti Atipempherere
Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Akukhalabe Wamoyo Kuti Atipempherere oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Chifukwa chake Iye amapulumutsa kwathunthu amene amabwera kwa Mulungu kudzera mwa Iyeyo. Iye ali ndi moyo nthawi zonse kuti adziwapempherera iwo.
Ndani amene angatipeze ife olakwa? Palibe. Khristu Yesu amene anafa, kuposera pamenepo, amene anaukitsidwa ndi moyo, amene ali kudzanja lamanja la Mulungu ndiye amene akutipempherera.
Pakuti Khristu sanalowe mʼmalo opatulika omangidwa ndi anthu amene anali chifaniziro cha malo enieniwo. Iye analowa kumwamba kwenikweniko kuti azionekera pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.
Inu Ana anga okondedwa, ndikukulemberani zimenezi kuti musachimwe. Koma wina akachimwa, tili nayo Nkhoswe yotinenera kwa Atate, Yesu Khristu, Wolungamayo.
“Ine sindikupempherera iwo okhawa, komanso amene adzandikhulupirira chifukwa cha uthenga wawo. Ndikuwapempherera kuti onsewa akhale amodzi. Monga Inu Atate muli mwa Ine ndi Ine mwa Inu, iwonso akhale mwa Ife kuti dziko lapansi likhulupirire kuti Inu munandituma Ine.
Motero Ine ndidzamupatsa ulemu pamodzi ndi akuluakulu, adzagawana zofunkha ndi ankhondo amphamvu, popeza anapereka moyo wake mpaka kufa, ndipo anamuyika mʼgulu la anthu olakwa kuti akhululukidwe. Pakuti iye anasenza machimo a anthu ambiri, ndipo anawapempherera anthu olakwa.
Pakuti Khristu sanalowe mʼmalo opatulika omangidwa ndi anthu amene anali chifaniziro cha malo enieniwo. Iye analowa kumwamba kwenikweniko kuti azionekera pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife. Iye sanalowe kumwamba kuti azikadziperekanso nsembe kachiwiri monga momwe mkulu wa ansembe ankachitira chaka ndi chaka ku Malo Opatulika kwambiri ndi magazi amene sanali ake.
Popeza kuti tili ndi Mkulu wa ansembe wopambana, amene analowa kale kumwamba, Yesu Mwana wa Mulungu, tiyeni tigwiritsitse chikhulupiriro chathu chimene timavomereza. Pakuti sitili ndi Mkulu wa ansembe amene sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofowoka zathu. Koma tili naye amene anayesedwa mʼnjira zonse monga ife, koma sanachimwe. Tiyeni tsono tiyandikire ku mpando waufumu, wachisomo mopanda mantha, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo chotithandiza pa nthawi yeniyeni.