Mavesi a m'Baibulo Onena za Kulanga mwa Chikondi

Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Kulanga mwa Chikondi oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Miyambo 13:24

Amene sakwapula mwana wake, ndiye kuti amamuda, koma wokonda mwana wake sazengereza kumulanga.

02 Miyambo 22:15

Uchitsiru umakhala mu mtima mwa mwana, koma ndodo yomulangira mwanayo idzachotsa uchitsiruwo.

03 Ahebri 12:11

Palibe chilango chimene chimaoneka kuti ndi chabwino pa nthawiyo, komatu chowawa. Koma pambuyo pake, chimabweretsa chipatso chachilungamo ndi mtendere kwa iwo amene aleredwa mwa njira imeneyi.

04 Miyambo 29:17

Umulange mwana wako ndipo adzakupatsa mtendere ndi kusangalatsa mtima wako.

05 Miyambo 3:11-12

Mwana wanga usanyoze malangizo a Yehova, ndipo usayipidwe ndi chidzudzulo chake. Paja Yehova amadzudzula amene amamukonda, monga abambo achitira mwana amene amakondwera naye.

06 Miyambo 19:18

Langa mwana wako, chiyembekezo chikanalipo; ngati sutero udzawononga moyo wake.

07 Chivumbulutso 3:19

Amene ndimawakonda ndimawadzudzula ndi kuwalanga. Choncho chita changu ndipo lapa.

Mitu yofanana