Mavesi a m'Baibulo Onena za Khama

Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Khama oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Miyambo 12:24

Ogwira ntchito mwakhama adzalamulira, koma aulesi adzakhala ngati kapolo.

02 Miyambo 10:4

Wochita zinthu mwaulesi amasauka, koma wogwira ntchito mwakhama amalemera.

03 Akolose 3:23

Chilichonse mungachite, muchite ndi mtima wanu onse, monga mmene mungagwirire ntchito ya Ambuye osati ya anthu.

04 Miyambo 13:4

Munthu waulesi amakhumbira zinthu koma sapeza kanthu, koma munthu wakhama adzalemera.

05 Mlaliki 9:10

Ntchito iliyonse imene ukuyigwira, uyigwire ndi mphamvu zako zonse, pakuti ku manda kumene ukupita kulibe kugwira ntchito, kulibe malingaliro, chidziwitso ndiponso nzeru.

06 Miyambo 21:5

Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa zinthu zake; koma aliyense wochita zinthu mofulumira amadzakhala wosauka.

07 Miyambo 22:29

Kodi ukumuona munthu waluso pa ntchito yake? Iye adzatumikira mafumu; sadzatumikira anthu wamba.

Mitu yofanana