Mavesi a m'Baibulo Onena za Kukhutira
Mavesi 5 a m'Baibulo onena za Kukhutira oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Sindikunena izi chifukwa choti ndikusowa thandizo, poti ine ndaphunzira kukhala wokwaniritsidwa ndi zimene ndili nazo.
Koma kulemekeza Mulungu kuli ndi phindu lalikulu. Pakuti sitinabweretse kanthu mʼdziko lapansi, ndipo sitingatengenso kanthu pochoka mʼdziko lapansi. Koma ngati tili ndi chakudya ndi zovala, zimenezi zitikwanire.
Mtima wanu usakonde ndalama koma mukhutitsidwe ndi zimene muli nazo, chifukwa Mulungu anati, “Sadzakusiyani, kapena kukutayani konse.”
Choyamba, mundichotsere kutali nane mabodza ndi chinyengo. Chachiwiri, ndisakhale mʼmphawi kapena munthu wachuma. Koma muzindidyetsa chakudya chondikwanira tsiku ndi tsiku kuopa kuti ndikakhuta kwambiri ndingayambe kukukanani, nʼkumanena kuti, ‘Yehova ndiye yaninso?’ Kuopanso kuti ndikakhala wosauka ndingayambe kuba, potero nʼkuyipitsa dzina la Mulungu wanga.”
Ndimadziwa kusauka nʼkutani, ndipo ndimadziwa kulemera nʼkutani. Ndaphunzira chinsinsi chokhala wokhutitsidwa mwa njira ina iliyonse, kaya nʼkudya bwino kapena kukhala ndi njala, kaya kukhala ndi chuma kapena umphawi. Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu.