Mavesi a m'Baibulo Onena za Ndalama
Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Ndalama oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Pakuti kukonda ndalama ndiye muzu wa zoyipa za mitundu yonse. Anthu ena ofunitsitsa ndalama, asochera ndipo asiya njira yachikhulupiriro ndipo adzitengera zowawitsa zambiri.
“Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri. Pakuti pena adzamuda mmodzi ndi kukonda winayo kapena adzagwira ntchito mokhulupirika kwa mmodzi, nadzanyoza winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa chuma pa nthawi imodzi.
Mtima wanu usakonde ndalama koma mukhutitsidwe ndi zimene muli nazo, chifukwa Mulungu anati, “Sadzakusiyani, kapena kukutayani konse.”
Uzilemekeza Yehova ndi chuma chako chonse; zokolola zonse zoyamba kucha uzilemekeza nazonso Yehova. Ukatero nkhokwe zako zidzadzaza ndi zinthu zambiri, ndiponso mitsuko yako idzadzaza ndi vinyo.
“Palibe wantchito amene angatumikire mabwana awiri. Mwina iye adzadana ndi wina ndi kukonda winayo, kapena adzakhala wodzipereka kwa wina ndi kumunyoza winayo. Inu simungathe kutumikira Mulungu komanso ndalama nthawi imodzi.”
Aliyense amene amadalira chuma chake adzafota, koma wolungama adzaphukira ngati tsamba lobiriwira.
Aliyense amene amakonda ndalama sakhutitsidwa ndi ndalamazo; aliyense amene amakonda chuma sakhutitsidwa ndi zimene amapeza. Izinso ndi zopandapake.
Kenaka Iye anawawuza kuti, “Chenjerani! Khalani tcheru ndi makhalidwe onse adyera; moyo wa munthu sukhala chifukwa cha kuchuluka kwa zimene ali nazo.”
Wolemera amalamulira wosauka, ndipo wokongola zinthu amakhala kapolo wa womukongozayo.
Anthu onse amene ali ndi chuma uwalamule kuti asanyade kapena kuyika mitima yawo pa chuma chimene nʼchosadalirika. Koma chiyembekezo chawo chikhale mwa Mulungu amene amatipatsa mowolowamanja zonse zotisangalatsa. Uwalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, owolowamanja ndi okonda kugawana zinthu zawo ndi anzawo.
“Musadziwunjikire chuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zimawononga ndi pamene mbala zimathyola ndi kuba. Koma mudziwunjikire chuma kumwamba kumene njenjete ndi dzimbiri siziwononga ndipo mbala sizithyola ndi kuba. Pakuti kumene kuli chuma chako, mtima wako udzakhala komweko.