Mavesi a m'Baibulo Onena za Ngongole

Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Ngongole oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Miyambo 22:7

Wolemera amalamulira wosauka, ndipo wokongola zinthu amakhala kapolo wa womukongozayo.

02 Aroma 13:8

Musakhale ndi ngongole ndi wina aliyense kupatula ngongole ya kukondana wina ndi mnzake. Pakuti amene amakonda munthu mnzake wakwaniritsa lamulo.

03 Miyambo 22:26-27

Usakhale munthu wopereka chikole kapena kukhala mboni pa ngongole; ngati ulephera kupeza njira yolipirira adzakulanda ngakhale bedi lako lomwe.

04 Masalimo 37:21

Oyipa amabwereka ndipo sabweza koma olungama amapereka mowolowamanja.

05 Deuteronomo 15:6

Pakuti Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani monga analonjeza, ndipo inu mudzabwereketsa chuma kwa mitundu yambiri ya anthu koma inu simudzabwereka kwa aliyense. Mudzalamulira mitundu yambiri ya anthu koma inuyo palibe amene adzakulamulireni.

06 Miyambo 3:27-28

Usaleke kuchitira zabwino amene ayenera kulandira zabwino, pamene uli nazo mphamvu zochitira zimenezi. Usanene kwa mnansi wako kuti, “Pita, uchite kubweranso. Ndidzakupatsa mawa” pamene uli nazo tsopano.

07 Masalimo 37:26

Iwo ndi owolowamanja nthawi zonse ndipo amabwereketsa mwaufulu; ana awo adzadalitsika.

08 2 Mafumu 4:7

Mayiyo anapita nakamuwuza munthu wa Mulungu amene anamuyankha kuti, “Pita, kagulitse mafutawo ndipo ukabweze ngongole ija. Ndalama zotsalazo zikakhale zako ndi ana ako.”

09 Mateyu 18:27

Bwana wakeyo anamuchitira chifundo, namukhululukira ngongoleyo ndipo anamulola apite.

Mitu yofanana