Mavesi a m'Baibulo Onena za Umphawi

Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Umphawi oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Miyambo 19:17

Amene amakomera mtima osauka amachita ngati wakongoletsa Yehova, ndipo Yehovayo ndiye adzamubwezere.

02 Miyambo 14:31

Amene amapondereza mʼmphawi amanyoza mlengi wake, koma wochitira chifundo munthu wosowa amalemekeza Mulungu.

03 Miyambo 22:2

Wolemera ndi wosauka ndi ofanana; onsewa anawalenga ndi Yehova.

04 1 Samueli 2:7

Yehova amasaukitsa ndipo amalemeretsa, amatsitsa ndipo amakweza.

05 Masalimo 140:12

Ndikudziwa kuti Yehova amapereka chiweruzo cholungama kwa anthu osauka, ndipo amateteza zolinga za anthu osowa.

06 Miyambo 30:8-9

Choyamba, mundichotsere kutali nane mabodza ndi chinyengo. Chachiwiri, ndisakhale mʼmphawi kapena munthu wachuma. Koma muzindidyetsa chakudya chondikwanira tsiku ndi tsiku kuopa kuti ndikakhuta kwambiri ndingayambe kukukanani, nʼkumanena kuti, ‘Yehova ndiye yaninso?’ Kuopanso kuti ndikakhala wosauka ndingayambe kuba, potero nʼkuyipitsa dzina la Mulungu wanga.”

07 Miyambo 13:23

Tsala la munthu wosauka limalola chakudya chambiri, koma anthu opanda chilungamo amachilanda.

08 Miyambo 17:5

Iye amene amalalatira mʼmphawi amanyoza mlengi wake; amene amakondwerera tsoka la mnzake sadzakhala osalangidwa.

09 Miyambo 31:20

Iye amachitira chifundo anthu osauka ndipo amapereka chithandizo kwa anthu osowa.

10 Luka 6:20

Akuyangʼana ophunzira ake, Iye anati, “Odala ndinu amene ndi osauka, chifukwa ufumu wa Mulungu ndi wanu.

11 Miyambo 21:13

Amene atsekera mʼkhutu mwake wosauka akamalira, nayenso adzalira koma palibe adzamuyankhe.

12 Miyambo 30:14

Pali ena amene mano awo ali ngati malupanga ndipo zibwano zawo zili ngati mipeni moti amadya amphawi ndi kuwachotsa pa dziko lapansi. Amachotsanso anthu osauka pakati pa anzawo.”

Mitu yofanana