Mavesi a m'Baibulo Onena za Kufuwulira kwa Mulungu

Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Kufuwulira kwa Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Masalimo 34:17

Olungama amafuwula, ndipo Yehova amawamva; Iye amawalanditsa ku mavuto awo onse.

02 Masalimo 18:6

Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova; ndinalirira kwa Mulungu wanga kuti andithandize. Ali mʼNyumba yake, anamva mawu anga; kulira kwanga kunafika pamaso pake ndi mʼmakutu mwake.

03 Masalimo 120:1

Ndimafuwulira kwa Yehova mʼmasautso anga, ndipo Iye amandiyankha.

04 Yona 2:2

Iye anati: “Pamene ndinali mʼmavuto anga ndinayitana Yehova, ndipo Iye anandiyankha. Ndili ku dziko la anthu akufa ndinapempha thandizo, ndipo Inu munamva kulira kwanga.

05 Masalimo 145:18

Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuyitana, onse amene amamuyitana Iye mʼchoonadi.

06 Masalimo 40:1

Mofatsa ndinadikira Yehova Iye anatembenukira kwa ine ndipo anamva kulira kwanga.

07 Masalimo 86:7

Pa tsiku la mavuto anga ndidzayitana Inu, pakuti Inu mudzandiyankha.

08 Masalimo 77:1

Ndinafuwulira Mulungu kupempha thandizo; ndinafuwula mokweza kwa Mulungu kuti anditcherere khutu.

Mitu yofanana