Mavesi a m'Baibulo Onena za Pempherani Mosalekeza

Mavesi 13 a m'Baibulo onena za Pempherani Mosalekeza oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 1 Atesalonika 5:17

Pempherani kosalekeza.

02 Akolose 4:2

Pempherani modzipereka, mukhale atcheru ndiponso oyamika.

03 Aefeso 6:18

Ndipo mupemphere mwa Mzimu nthawi zonse, mʼmitundu yonse ya mapemphero ndi zopempha. Ndipo pozindikira izi, khalani achangu kupempherera oyera mtima nthawi zonse.

04 Luka 18:1

Kenaka Yesu anawuza ophunzira ake fanizo kuwaonetsa kuti iwo ayenera kumapemphera nthawi zonse ndikuti asafowoke.

05 Aroma 12:12

Kondwerani mʼchiyembekezo, pirirani mʼmasautso ndiponso khulupirikani mʼpemphero.

Onsewa ndi mtima umodzi anapitiriza kupemphera pamodzi ndi amayi, ndi Mariya amayi ake a Yesu, ndiponso abale ake a Yesu.

Iwo ankasonkhana pamodzi kuphunzitsidwa ndi atumwi, pachiyanjano, pachakudya ndi popemphera.

08 Danieli 6:10

Danieli atamva kuti lamulo lasindikizidwa, anapita ku nyumba kwake nalowa mʼchipinda chapamwamba chimene mazenera ake anali otsekula kuloza ku Yerusalemu. Katatu pa tsiku iye ankagwada pansi pa mawondo ndipo amapemphera, kuyamika Mulungu wake, monga momwe ankachitira kale.

09 Masalimo 55:17

Madzulo, mmawa ndi masana ndimalira mowawidwa mtima, ndipo Iye amamva mawu anga.

10 1 Mbiri 16:11

Dalirani Yehova ndi mphamvu zake; funafunani nkhope yake nthawi zonse.

11 Afilipi 4:6

Musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa china chilichonse, mwa pemphero ndi chidandaulo pamodzi ndi chiyamiko, perekani zopempha zanu kwa Mulungu.

Koma ife tidzadzipereka kuti tizipemphera ndi kulalikira mawu.”

13 Aroma 1:9

Mulungu amene ndimamutumikira ndi mtima wanga onse polalikira Uthenga Wabwino wa Mwana wake, ndi mboni yanga kuti ndimakupemphererani nthawi zonse.

Mitu yofanana