Mavesi a m'Baibulo Onena za Kupemphera Malemba

Mavesi 15 a m'Baibulo onena za Kupemphera Malemba oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Yohane 15:7

Ngati inu mukhala mwa Ine ndipo mawu anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene mukufuna ndipo mudzapatsidwa.

02 Masalimo 119:18

Tsekulani maso anga kuti ndithe kuona zinthu zodabwitsa mʼmalamulo anu.

03 Yesaya 55:11

Ndi mmenenso amachitira mawu ochokera mʼkamwa mwanga. Sadzabwerera kwa Ine kopanda phindu lake, koma adzachita zonse zimene ndifuna, ndipo adzakwaniritsa cholinga chimene ndinawatumira.

04 Akolose 3:16

Mawu a Khristu akhazikike kwathunthu mʼmitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana wina ndi mnzake ndi nzeru zonse pamene mukuyimba Masalimo, nyimbo zotamanda ndi nyimbo zauzimu, kuyimbira Mulungu ndi mitima yoyamika.

05 Ahebri 4:12

Paja Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amalowa mpaka molumikizirana moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana fundo ndi mafuta a mʼmafupa. Amaweruza malingaliro ndi zokhumba za mʼmitima.

06 Masalimo 119:105

Mawu anu ndi nyale ya kumapazi kwanga ndi kuwunika kwa pa njira yanga.

07 Masalimo 119:11

Ndasunga mawu anu mu mtima mwanga kuti ndisakuchimwireni.

08 2 Timoteyo 3:16

Malemba onse anawalembetsa ndi Mulungu, ndipo othandiza pophunzitsa, podzudzula, pokonza cholakwika ndi polangiza za chilungamo

09 Yoswa 1:8

Uziwerenga Buku la Malamuloli, uzilingalira zolembedwa mʼmenemo usana ndi usiku, kuti uchite zonse zimene zinalembedwamo. Ukamatero udzapeza bwino ndi kupambana.

10 Mateyu 4:4

Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa, ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Mulungu.’ ”

11 Yohane 8:31-32

Kwa Ayuda amene anamukhulupirira, Yesu anati, “Ngati inu mutsatira chiphunzitso changa, ndithu ndinu ophunzira anga. Tsono mudzadziwa choonadi, ndipo choonadicho chidzakumasulani.”

12 Masalimo 1:2

Koma chikondwerero chake chili mʼmalamulo a Yehova ndipo mʼmalamulo akewo amalingaliramo usana ndi usiku.

13 Deuteronomo 11:18

Sungani mawu amenewa mu mtima mwanu ndi mʼmaganizo mwanu, muwamangirire pa mikono yanu ndipo muwayike pamphumi panu.

14 Aroma 10:17

Motero, chikhulupiriro chimabwera pamene timva uthenga ndipo uthenga umamveka kuchokera ku mawu a Khristu.

15 Masalimo 19:14

Mawu a mʼkamwa mwanga ndi zolingalira za mu mtima mwanga zikhale zokondweretsa pamaso panu, Inu Yehova, Thanthwe langa ndi Mpulumutsi wanga.

Mitu yofanana