Mavesi a m'Baibulo Onena za Pemphero
Pemphero ndi mpweya wa moyo wachikhristu — kulankhula ndi Mulungu amene amamva ndi kuyankha. Musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa zonse mwa pemphero ndi pembedzero pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mavesi awa amakuyitana kuti upemphere molimba mtima ndi kupuma.
Musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa china chilichonse, mwa pemphero ndi chidandaulo pamodzi ndi chiyamiko, perekani zopempha zanu kwa Mulungu.
Tsono choyamba ndikukupemphani kuti mupempherere anthu onse. Mapemphero anu akhale opemba, opempha, opempherera ena ndi oyamika.
Kenaka Yesu anawuza ophunzira ake fanizo kuwaonetsa kuti iwo ayenera kumapemphera nthawi zonse ndikuti asafowoke.
Ngati inu mukhala mwa Ine ndipo mawu anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene mukufuna ndipo mudzapatsidwa.
Olungama amafuwula, ndipo Yehova amawamva; Iye amawalanditsa ku mavuto awo onse.
Mpaka liti Yehova? Kodi mudzandiyiwala mpaka kalekale? Mpaka liti mudzandibisira nkhope yanu?
Tiyeni tsono tiyandikire ku mpando waufumu, wachisomo mopanda mantha, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo chotithandiza pa nthawi yeniyeni.
“Pemphani ndipo mudzapatsidwa; funafunani ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsekulirani.
Ndipo pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa munthu wodwalayo ndipo Ambuye adzamuutsa. Ngati wachimwa adzakhululukidwa.
Koma inu okondedwa, muthandizane kuti mukule pa chikhulupiriro chanu choyera, ndipo muzipemphera ndi mphamvu ya Mzimu Woyera.
Choncho, ululiranani machimo anu ndi kupemphererana wina ndi mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama ndi lamphamvu ndipo limagwira ntchito.
Koma pamene mupemphera, lowani mʼchipinda chanu chamʼkati, ndi kutseka chitseko ndipo mupemphere kwa Atate anu amene saoneka. Ndipo Atate anu, amene amaona zochitika mseri, adzakupatsani mphotho.
“Komanso ndikukuwuzani inu kuti ngati awiri a inu pa dziko lapansi avomerezana kanthu kalikonse kamene mukapempha, Atate anga akumwamba adzakuchitirani.