Mavesi a m'Baibulo Onena za Mukamapemphera
Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Mukamapemphera oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Koma pamene mupemphera, lowani mʼchipinda chanu chamʼkati, ndi kutseka chitseko ndipo mupemphere kwa Atate anu amene saoneka. Ndipo Atate anu, amene amaona zochitika mseri, adzakupatsani mphotho.
Ndipo pamene mukupemphera, musamabwerezabwereza monga akunja, pakuti iwo amaganiza kuti adzamveka chifukwa chochulutsa mawu.
“Chifukwa chake pempherani motere: “ ‘Atate athu akumwamba, dzina lanu lilemekezedwe, Ufumu wanu ubwere, chifuniro chanu chichitike pansi pano monga kumwamba. Mutipatse chakudya chathu chalero. Mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso tawakhululukira amangawa athu. Ndipo musatitengere kokatiyesa; koma mutipulumutse kwa woyipayo.’
Kenaka Yesu anawuza ophunzira ake fanizo kuwaonetsa kuti iwo ayenera kumapemphera nthawi zonse ndikuti asafowoke.
Mmamawa, kukanali kamdima, Yesu anadzuka, nachoka pa nyumbapo kupita kumalo kwa yekha, kumene anakapemphera.
“Pamene mupemphera, musakhale ngati achiphamaso, chifukwa iwo amakonda kupemphera choyimirira mʼmasunagoge ndi pa mphambano za mʼmisewu kuti anthu awaone. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwo alandiriratu mphotho yawo yonse.
Musakhale ngati iwo chifukwa Atate anu amadziwa zimene musowa musanapemphe.
Tsiku lina Yesu amapemphera pamalo ena. Atamaliza, mmodzi wa ophunzira ake anati kwa Iye, “Ambuye tiphunzitseni kupemphera, monga momwe Yohane anaphunzitsira ophunzira ake.”