Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuvomerezana M'pemphero

Mavesi 6 a m'Baibulo onena za Kuvomerezana M'pemphero oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Mateyu 18:19

“Komanso ndikukuwuzani inu kuti ngati awiri a inu pa dziko lapansi avomerezana kanthu kalikonse kamene mukapempha, Atate anga akumwamba adzakuchitirani.

02 Mateyu 18:20

Pakuti pamene awiri kapena atatu asonkhana pamodzi mʼdzina langa, Ine ndili nawo pomwepo.”

Onsewa ndi mtima umodzi anapitiriza kupemphera pamodzi ndi amayi, ndi Mariya amayi ake a Yesu, ndiponso abale ake a Yesu.

Iwo ankasonkhana pamodzi kuphunzitsidwa ndi atumwi, pachiyanjano, pachakudya ndi popemphera.

Anthu atamva zimenezi anafuwula ndi mtima umodzi napemphera kwa Mulungu. Iwo anati, “Ambuye wolamulira zonse, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndiponso zonse zili mʼmenemo.

Kotero Petro anasungidwa mʼndende, koma mpingo unamupempherera kolimba kwa Mulungu.

Mitu yofanana