Mavesi a m'Baibulo Onena za Kupemphera Mwa Mzimu

Mavesi 15 a m'Baibulo onena za Kupemphera Mwa Mzimu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Yuda 1:20

Koma inu okondedwa, muthandizane kuti mukule pa chikhulupiriro chanu choyera, ndipo muzipemphera ndi mphamvu ya Mzimu Woyera.

02 Aroma 8:26

Momwemonso, Mzimu amatithandiza ife mʼkufowoka kwathu. Ife sitidziwa momwe tiyenera kupempherera koma Mzimu mwini amatipempherera mobuwula ndi mawu osafotokozedwa.

03 Aefeso 6:18

Ndipo mupemphere mwa Mzimu nthawi zonse, mʼmitundu yonse ya mapemphero ndi zopempha. Ndipo pozindikira izi, khalani achangu kupempherera oyera mtima nthawi zonse.

04 1 Akorinto 14:15

Tsono pamenepa nʼkutani? Ndidzapemphera ndi mzimu wanga, komanso ndidzapemphera ndi nzeru zanga. Ndidzayimba ndi mzimu wanga, komanso ndidzayimba ndi nzeru zanga.

05 Agalatiya 4:6

Ndipo popeza ndinu ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake kuti alowe mʼmitima mwathu, Mzimu amene amafuwula kuti, “Abba, Atate.”

06 Aroma 8:27

Koma Iye amene amasanthula mitima yathu amadziwa maganizo a Mzimu, chifukwa Mzimu amapempherera oyera mtima molingana ndi chifuniro cha Mulungu.

07 1 Akorinto 14:14

Popeza ngati ndipemphera mʼmalilime, ndi mzimu wanga umene ukupemphera, koma nzeru zanga sizikupindula kanthu.

08 Yohane 4:23-24

Koma nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano pamene opembedza woona adzapembedza Atate mu mzimu ndi mʼchoonadi, pakuti opembedza otere ndiwo amene Atate akuwafuna. Mulungu ndi Mzimu, ndipo omupembedza Iye ayenera kumupembedza mu mzimu ndi mʼchoonadi.”

09 Zekariya 12:10

“Ndipo pa nyumba ya Davide ndi pa anthu okhala mu Yerusalemu ndidzakhuthulirapo mzimu wachisomo ndi wopemphera. Iwo adzandiyangʼana Ine, amene anamubaya, ndipo adzamulirira kwambiri monga momwe munthu amalirira mwana wake mmodzi yekhayo, ndiponso adzamva chisoni kwambiri monga momwe amachitira ndi mwana woyamba kubadwa.

Iwo atatha kupemphera, malo amene anasonkhanapo anagwedezeka. Ndipo iwo onse anadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo anayankhula Mawu a Mulungu molimba mtima.

11 Afilipi 3:3

Pakuti ochita mdulidwe weniweni ndife. Ife amene timatumikira Mulungu motsogozedwa ndi Mzimu. Ife amene timanyadira Khristu, ndipo sitidalira zinthu za thupi

12 1 Akorinto 14:16

Ngati mutamanda Mulungu mu mzimu, kodi munthu amene wapezeka pakati pa amene akuyankhula zomwe sakumva, adzavomereza bwanji kuti “Ameni” pa pemphero lanu loyamikalo popeza sakumva chimene mukunena?

13 Aroma 8:15

Mzimu amene inu munalandira samakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha, koma Mzimu amakusandutsani ana. Ndipo mwa Iye ife timafuwula kuti, “Abba, Atate.”

14 Agalatiya 5:25

Popeza timakhala ndi moyo mwa Mzimu Woyera, tiyeni tiyende pamodzi ndi Mzimu Woyera.

15 Yuda 1:20-21

Koma inu okondedwa, muthandizane kuti mukule pa chikhulupiriro chanu choyera, ndipo muzipemphera ndi mphamvu ya Mzimu Woyera. Khalani mʼchikondi cha Mulungu pamene mukudikira chifundo cha Ambuye athu Yesu Khristu kuti akubweretsereni moyo wosatha.

Mitu yofanana