Mavesi a m'Baibulo Onena za Anapachikidwa Chifukwa cha Ife
Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Anapachikidwa Chifukwa cha Ife oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Ndinapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano mʼthupi lino, ndi moyo mwachikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu, amene anandikonda nadzipereka yekha chifukwa cha ine.
Koma Mulungu anaonetsa chikondi chake kwa ife chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu anatifera.
Iye mwini anasenza machimo athu mʼthupi lake pa mtanda, kuti ife tife kutchimo ndi kukhala ndi moyo potsata chilungamo, ndipo ndi mabala ake munachiritsidwa.
Khristu anatiwombola ku temberero la lamulo pokhala temberero mʼmalo mwathu, pakuti analemba kuti, “Aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa.”
koma ife timalalikira Khristu wopachikidwa. Chitsa chokhumudwitsa kwa Ayuda ndi chopusa kwa a mitundu ina.
Pakuti Khristu anafa chifukwa cha machimo kamodzi kokha kufera onse, wolungama kufera osalungama, kuti akufikitseni kwa Mulungu. Anaphedwa ku thupi koma anapatsidwa moyo mu mzimu.
Chifukwa cha ife, Mulungu anasandutsa wopanda tchimoyo kukhala tchimo, kuti mwa Iye ife tikakhale chilungamo cha Mulungu.
Anafafaniza kalata ya ngongole yathu, pomwe panali milandu yotitsutsa ife. Iye anayichotsa, nayikhomera pa mtanda.