Mavesi a m'Baibulo Onena za Kupambana mwa Khristu
Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Kupambana mwa Khristu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Koma tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Ayi, mu zonsezi ife ndife oposa agonjetsi mwa Iye amene anatikonda.
chifukwa aliyense amene ndi mwana wa Mulungu amagonjetsa dziko lapansi. Chikhulupiriro chathu ndicho timagonjetsera dziko lapansi.
Koma tithokoze Mulungu amene amatitsogolera nthawi zonse monga ogwidwa ku nkhondo a Khristu pa chipambano chake. Tsono amatigwiritsa ntchito yofalitsa ponseponse nzeru zodziwira Khristu ngati fungo labwino.
Pamene thupi lovundali likadzasanduka losavunda, ndipo thupi lotha kufali likadzasanduka losatha kufa, pamenepo zidzakwaniritsidwa zimene zinalembedwa zakuti, “Imfa yogonjetsedwa kwathunthu.” “Iwe imfa, kupambana kwako kuli kuti? Iwe imfa, ululu wako uli kuti?”
Nanga tsono tidzanena chiyani pa izi? Ngati Mulungu ali mbali yathu, adzatitsutsa ife ndani?
chifukwa aliyense amene ndi mwana wa Mulungu amagonjetsa dziko lapansi. Chikhulupiriro chathu ndicho timagonjetsera dziko lapansi. Ndani amagonjetsa dziko lapansi? Yekhayo amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu.