Mavesi a m'Baibulo Onena za Yehova Mtendere Wathu

Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Yehova Mtendere Wathu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Oweruza 6:24

Choncho Gideoni anamanga guwa lansembe la Yehova pamenepo ndipo analitcha kuti, Yehova ndiye mtendere. Kufikira lero lino guwali lilipo ku Ofura wa Mwabiezeri.

02 Yesaya 9:6

Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife, ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake. Ndipo adzamutcha dzina lake lakuti Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, ndi Mfumu ya Mtendere.

03 Yohane 14:27

Ine ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Ine sindikukupatsani monga dziko lapansi limaperekera. Mtima wanu usavutike ndipo musachite mantha.

04 Afilipi 4:7

Ndipo mtendere wa Mulungu, umene upambana nzeru zonse udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

05 Aroma 5:1

Tsopano popeza tayesedwa olungama mwa chikhulupiriro, tili ndi mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.

06 Yesaya 26:3

Inu mudzamupatsa munthu wa mtima wokhazikika mtendere weniweni.

07 Numeri 6:24-26

“ ‘Yehova akudalitse ndi kukusunga; Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, nakuchitira chisomo; Yehova akweze nkhope yake pa iwe, nakupatse mtendere.’ ”

08 2 Atesalonika 3:16

Tsopano Ambuye mwini mtendere akupatseni mtendere nthawi zonse mwa njira iliyonse. Ambuye akhale ndi inu nonse.

09 Akolose 3:15

Mtendere wa Khristu ulamulire mʼmitima mwanu, popeza monga ziwalo za thupi limodzi, munayitanidwa kuti mukhale ndi mtendere. Ndipo muziyamika.

10 Aefeso 2:14

Pakuti Iye mwini ndiye mtendere wathu, amene anachita kuti awiri akhale mmodzi ndipo anagumula chotchinga, khoma la udani lotilekanitsa,

11 Yesaya 53:5

Koma iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, ndipo anamuzunza chifukwa cha zoyipa zathu; iye analangidwa kuti ife tikhale ndi mtendere, ndipo ndi mabala ake ife tinachiritsidwa.

Mitu yofanana