Mavesi a m'Baibulo Onena za Temberero Lachotsedwa

Mavesi 7 a m'Baibulo onena za Temberero Lachotsedwa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Agalatiya 3:13

Khristu anatiwombola ku temberero la lamulo pokhala temberero mʼmalo mwathu, pakuti analemba kuti, “Aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa.”

02 Aroma 8:1

Choncho, tsopano amene ali mwa Khristu Yesu alibe mlandu owatsutsa

03 Akolose 2:14

Anafafaniza kalata ya ngongole yathu, pomwe panali milandu yotitsutsa ife. Iye anayichotsa, nayikhomera pa mtanda.

04 1 Petro 2:24

Iye mwini anasenza machimo athu mʼthupi lake pa mtanda, kuti ife tife kutchimo ndi kukhala ndi moyo potsata chilungamo, ndipo ndi mabala ake munachiritsidwa.

05 Chivumbulutso 22:3

Sipadzakhalanso temberero lililonse. Mpando waufumu wa Mulungu ndi wa Mwana Wankhosa udzakhala mu mzindawo, ndipo atumiki ake adzamutumikira.

06 Chivumbulutso 21:4

‘Mulungu adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo. Sikudzakhalanso imfa kapena kukhuza maliro kapena kulira kapena ululu popeza zakale zapita.’ ”

07 2 Akorinto 5:21

Chifukwa cha ife, Mulungu anasandutsa wopanda tchimoyo kukhala tchimo, kuti mwa Iye ife tikakhale chilungamo cha Mulungu.

Mitu yofanana