Mavesi a m'Baibulo Onena za Utumiki

Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Utumiki oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Marko 10:45

Pakuti ngakhale Mwana wa Munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira, ndi kupereka moyo wake kuti ukhale dipo la anthu ambiri.”

02 Mateyu 20:28

Momwenso Mwana wa Munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira, ndi kupereka moyo wake kukhala dipo la anthu ambiri.”

03 Yohane 13:15

Ine ndakupatsani chitsanzo kuti muzichita monga Ine ndachitira.

04 Afilipi 2:7

Koma anadzichepetsa kotheratu nakhala ndi khalidwe ngati la kapolo ndi kukhala munthu ngati anthu ena onse.

05 Agalatiya 5:13

Inu abale, Mulungu anakuyitanani kuti mukhale mfulu. Koma musagwiritse ntchito ufulu wanuwo kuchita zoyipa zachikhalidwe cha uchimo cha thupi lanu, koma mutumikirane wina ndi mnzake mwachikondi.

06 Mateyu 23:11

Wamkulu pakati panu adzakhala wokutumikirani.

07 1 Petro 4:10

Aliyense agwiritse ntchito mokhulupirika mphatso iliyonse imene anayilandira potumikira ena ngati adindo ogwiritsa bwino ntchito mphatso za Mulungu za mitundumitundu.

08 Marko 9:35

Atakhala pansi, Yesu anayitana khumi ndi awiriwo nati, “Ngati wina aliyense afuna kukhala woyamba, ayenera kukhala wotsiriza ndi wotumikira onse.”

09 Luka 22:27

Pakuti wamkulu ndani, iye amene ali pa tebulo kapena iye amene akutumikira? Kodi si iye amene ali pa tebulo? Koma ndili pakati panu ngati mmodzi wokutumikirani.

10 Yoswa 24:15

Koma ngati kutumikira Yehova kukuyipirani, sankhani lero amene mudzamutumikire, kapena milungu imene makolo anu ankayitumikira kutsidya kwa mtsinje wa Yufurate, kapena milungu ya Aamori, amene mukukhala mʼdziko lawo. Koma ine ndi banja langa, tidzatumikira Yehova.”

11 Akolose 3:23-24

Chilichonse mungachite, muchite ndi mtima wanu onse, monga mmene mungagwirire ntchito ya Ambuye osati ya anthu. Inu mukudziwa kuti mudzalandira mphotho monga cholowa kuchokera kwa Ambuye. Ndi Ambuye Khristu amene mukumutumikira.

Mitu yofanana