Mavesi a m'Baibulo Onena za Kuika Ena Patsogolo
Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Kuika Ena Patsogolo oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Musamangofuna zokomera inu nokha koma aliyense azifuna zokomeranso ena.
Mukondane kwathunthu monga abale. Lemekezanani wina ndi mnzake kuposa inu eni.
Munthu aliyense asafunefune zokomera iye yekha, koma zokomeranso ena.
Musachite kalikonse ndi mtima odzikonda chabe kapena odzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa ndipo aliyense aziona mnzake ngati womuposa iyeyo.
Thandizanani kusenza zolemetsa zanu, ndipo mʼnjira imeneyi mudzakwanitsa lamulo la Khristu.
Chikondi chilibe mwano, sichodzikonda, sichipsa mtima msanga, sichisunga mangawa.
Ife amene tili ndi chikhulupiriro champhamvu tiziwalezera mtima anthu ofowoka, ndipo tisamadzikondweretse tokha. Aliyense wa ife akondweretse mnzake pomuchitira zabwino zomulimbikitsa.
Atakhala pansi, Yesu anayitana khumi ndi awiriwo nati, “Ngati wina aliyense afuna kukhala woyamba, ayenera kukhala wotsiriza ndi wotumikira onse.”
Palibe munthu ali ndi chikondi choposa ichi, choti munthu nʼkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.
Pa ubale wanu wina ndi mnzake, mukhale ndi mtima wofanana ndi wa Khristu Yesu: Iyeyu, pokhala Mulungu ndithu, sanatenge kufanana ndi Mulungu kukhala chinthu choyenera kuchigwiritsa. Koma anadzichepetsa kotheratu nakhala ndi khalidwe ngati la kapolo ndi kukhala munthu ngati anthu ena onse.
Mu zonse ndikuyesetsa kukondweretsa aliyense mʼnjira iliyonse. Popeza sindikufunafuna zokondweretsa ine ndekha koma zokomera ambiri kuti apulumutsidwe.
Muyanjane wina ndi mnzake. Musakhale onyada, koma lolani kuyanjana ndi anthu wamba. Musaganize kuti mumadziwa zonse.