Mavesi a m'Baibulo Onena za Kudzichepetsa

Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Kudzichepetsa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Afilipi 2:3

Musachite kalikonse ndi mtima odzikonda chabe kapena odzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa ndipo aliyense aziona mnzake ngati womuposa iyeyo.

02 Yakobo 4:6

Koma amatipatsa chisomo chochuluka. Nʼchifukwa chake Malemba amati, “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma apereka chisomo kwa odzichepetsa.”

03 Miyambo 22:4

Mphotho ya munthu wodzichepetsa ndi woopa Yehova ndi chuma, ulemu ndi moyo.

04 Mika 6:8

Munthu iwe, Yehova wakuonetsa kale chimene chili chabwino. Tsono kodi Yehova akuyembekezera chiyani kwa iwe? Uzichita zolungama ndi kukonda chifundo ndiponso kuyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.

05 Aroma 12:3

Chifukwa cha chisomo chopatsidwa kwa ine, ndinena kwa aliyense wa inu kuti musadziyenereze nokha kuposa mmene mulili. Koma mudziganizire nokha modzichepetsa, molingana ndi muyeso wa chikhulupiriro chimene Mulungu wakupatsani.

06 1 Petro 5:5

Momwemonso, inu anyamata gonjerani amene ndi akulu. Inu nonse mukhale odzichepetsa kuti mutumikirane, chifukwa, “Mulungu amatsutsana nawo odzikuza, koma amapereka chisomo kwa odzichepetsa.”

07 Miyambo 11:2

Kunyada kukalowa, pamafikanso manyazi, koma pamene pali kudzichepetsa pameneponso pali nzeru.

08 Miyambo 15:33

Kuopa Yehova kumaphunzitsa munthu nzeru, ndipo kudzichepetsa ndi ulemu chili patsogolo ndi kudzichepetsa.

09 Akolose 3:12

Choncho, ngati anthu osankhidwa ndi Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa kwambiri, muvale chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa ndi kupirira.

Mitu yofanana