Mavesi a m'Baibulo Onena za Mulungu Amakweza Odzichepetsa

Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Mulungu Amakweza Odzichepetsa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 1 Petro 5:6

Choncho, mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthawi yake adzakukwezeni.

02 Yakobo 4:10

Dzichepetseni pamaso pa Ambuye ndipo Iye adzakukwezani.

03 Luka 14:11

Pakuti aliyense wodzikuza adzamuchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamukweza.”

04 Mateyu 23:12

Pakuti aliyense amene adzikuza adzachepetsedwa, ndipo aliyense amene adzichepetsa adzakuzidwa.

05 Miyambo 29:23

Kunyada kwa munthu kudzamutsitsa, koma munthu wodzichepetsa amalandira ulemu.

06 Mateyu 18:4

Chifukwa chake, aliyense amene adzichepetsa yekha ngati kamwana aka, ameneyo ndiye wamkulu koposa onse mu ufumu wakumwamba.

07 Masalimo 138:6

Ngakhale kuti Yehova ngokwezeka, amasamalira odzichepetsa, koma anthu onyada amawadziwira chapatali.

08 Miyambo 18:12

Chiwonongeko chisanafike, mtima wa munthu umakhala wonyada, koma ulemu umatsatira kudzichepetsa.

09 Yesaya 57:15

Pakuti Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthawi zonse, amene dzina lake ndi Woyerayo, akunena kuti, “Ndimakhala pamalo aulemu ndi opatulika, koma ndimakhalanso ndi munthu wodzichepetsa ndi wosweka mtima kuti odzichepetsawo ndiwalimbitse ndi kuwachotsa mantha osweka mtima.

10 Luka 1:52

Iye anachotsa olamulira pa mipando yawo yaufumu, koma wakweza odzichepetsa.

11 Miyambo 22:4

Mphotho ya munthu wodzichepetsa ndi woopa Yehova ndi chuma, ulemu ndi moyo.

12 Masalimo 147:6

Yehova amagwiriziza anthu odzichepetsa, koma amagwetsa pansi anthu oyipa.

13 Yakobo 4:6

Koma amatipatsa chisomo chochuluka. Nʼchifukwa chake Malemba amati, “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma apereka chisomo kwa odzichepetsa.”

14 Luka 18:14

“Ine ndikukuwuzani kuti munthu wolandira msonkhoyu, osati Mfarisiyu, anapita kwawo atalungamitsidwa pamaso pa Mulungu. Chifukwa chake, aliyense wodzikweza adzachepetsedwa, ndipo wodzichepetsa adzakwezedwa.”

Mitu yofanana