Mavesi a m'Baibulo Onena za Kufatsa

Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Kufatsa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Afilipi 4:5

Kufatsa kwanu kuzioneka pamaso pa anthu onse. Ambuye anu ali pafupi.

02 Agalatiya 5:22-23

Koma chipatso cha Mzimu Woyera ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndi kudziretsa. Palibe lamulo loletsa zimenezi.

03 Akolose 3:12

Choncho, ngati anthu osankhidwa ndi Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa kwambiri, muvale chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa ndi kupirira.

04 Miyambo 15:1

Kuyankha kofatsa kumathetsa mkwiyo, koma mawu ozaza amautsa ukali.

05 2 Timoteyo 2:24

Ndiponso mtumiki wa Ambuye asamakangane ndi anthu, koma azikhala wachifundo kwa aliyense, wodziwa kuphunzitsa, osati wokalipakalipa.

06 Tito 3:2

Asamachitire chipongwe aliyense, asamakangane, akhale ofatsa ndipo oganizira ena, ndipo nthawi zonse akhale aulemu kwa anthu onse.

07 1 Petro 3:15

Koma lemekezani Khristu mʼmitima mwanu ngati Ambuye wanu. Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense amene akufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho.

08 Mateyu 11:29

Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa. Ndipo inu mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.

09 Aefeso 4:2

Mukhale odzichepetsa kwathunthu ndi ofatsa; mukhale oleza mtima, ololerana wina ndi mnzake mwachikondi.

10 1 Timoteyo 6:11

Koma iwe, munthu wa Mulungu, thawa zinthu zonsezi. Tsatira chilungamo, moyo wolemekeza Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, kupirira ndi kufatsa.

11 Yakobo 3:17

Koma nzeru imene imachoka kumwamba, poyamba ndi yangwiro, ndi yokonda mtendere, yoganizira za ena, yogonjera, yodzaza ndi chifundo ndi chipatso chabwino, yosakondera ndi yoona mtima.

12 Miyambo 25:15

Kupirira ndiye kumagonjetsa mfumu, ndipo kufewa mʼkamwa kutha kumafatsitsa munthu wowuma mtima.

13 1 Atesalonika 2:7

Ngati atumwi a Khristu tikanatha kukhala cholemetsa kwa inu, mʼmalo mwake tinali ngati ana aangʼono pakati panu. Monga mmene amayi amasamalira ana awo angʼono,

14 Yesaya 40:11

Iye adzasamalira nkhosa zake ngati mʼbusa: Iye adzasonkhanitsa ana ankhosa aakazi mʼmanja mwake ndipo Iye akuwanyamula pachifuwa chake ndi kutsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.

Mitu yofanana