Mavesi a m'Baibulo Onena za Kudzichepetsa

Mavesi 5 a m'Baibulo onena za Kudzichepetsa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Yakobo 4:10

Dzichepetseni pamaso pa Ambuye ndipo Iye adzakukwezani.

02 Miyambo 16:19

Nʼkwabwino kukhala ndi mtima wodzichepetsa pakati pa anthu oponderezedwa, kusiyana ndi kugawana zolanda ndi anthu onyada.

03 Yesaya 57:15

Pakuti Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthawi zonse, amene dzina lake ndi Woyerayo, akunena kuti, “Ndimakhala pamalo aulemu ndi opatulika, koma ndimakhalanso ndi munthu wodzichepetsa ndi wosweka mtima kuti odzichepetsawo ndiwalimbitse ndi kuwachotsa mantha osweka mtima.

04 Mateyu 23:12

Pakuti aliyense amene adzikuza adzachepetsedwa, ndipo aliyense amene adzichepetsa adzakuzidwa.

05 Luka 14:11

Pakuti aliyense wodzikuza adzamuchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamukweza.”

Mitu yofanana