Mavesi a m'Baibulo Onena za Okonzeka Kupereka Yankho

Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Okonzeka Kupereka Yankho oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 1 Petro 3:15

Koma lemekezani Khristu mʼmitima mwanu ngati Ambuye wanu. Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense amene akufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho.

02 Akolose 4:6

Mayankhulidwe anu nthawi zonse akhale odzaza ndi chisomo ndi okoma, kuti mudziwe kuyankha aliyense.

03 2 Timoteyo 4:2

Lalikira Mawu; khala wokonzeka pa nthawi yake, ngakhale pamene si pa nthawi yake. Konza zolakwa zawo, dzudzula ndipo limbikitsa moleza mtima kwambiri ndi malangizo osamalitsa.

04 Yuda 1:3

Okondedwa, ngakhale ndinkafunitsitsa kukulemberani za chipulumutso cha tonsefe, ndakakamizidwa kuti ndikulembereni ndi kukupemphani kolimba kuti mumenye ndithu nkhondo yotchinjiriza chikhulupiriro chimene Mulungu anachipereka kamodzi kokha kwa anthu onse oyera mtima.

05 Mateyu 10:32

“Aliyense amene avomereza Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzavomereza pamaso pa Atate anga akumwamba.

06 1 Petro 3:16

Koma chitani zimenezi mofatsa ndi mwaulemu, mukhale ndi chikumbumtima chosakutsutsani, kuti anthu ena akanena zoyipa za makhalidwe anu abwino mwa Khristu, achite okha manyazi ndi chipongwe chawocho.

Paulo, monga mwachizolowezi chake, analowa mʼsunagoge, ndipo anakambirana nawo Mawu a Mulungu kwa masabata atatu, kuwafotokozera ndi kuwatsimikizira kuti Khristu anayenera kufa ndi kuuka. Iye anati, “Yesu amene ndikukulalikirani ndiye Khristu.”

08 Tito 1:9

Iye ayenera kugwiritsa mawu okhulupirika monga tinaphunzitsira, kuti athe kulimbikitsa ena ndi chiphunzitso choona ndiponso kugonjetsa amene atsutsana nacho.

Mitu yofanana