Mavesi a m'Baibulo Onena za Olengezedwa Osalakwa
Mavesi 10 a m'Baibulo onena za Olengezedwa Osalakwa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Ndani amene adzabweretsa mlandu kutsutsa amene Mulungu anawasankha? Ndi Mulungu amene amalungamitsa.
Ndani amene angatipeze ife olakwa? Palibe. Khristu Yesu amene anafa, kuposera pamenepo, amene anaukitsidwa ndi moyo, amene ali kudzanja lamanja la Mulungu ndiye amene akutipempherera.
Choncho, tsopano amene ali mwa Khristu Yesu alibe mlandu owatsutsa
Wondikhalira kumbuyo ali pafupi, ndaninso amene adzandiyimba mlandu? Abwere kuti tionane maso ndi maso! Mdani wanga ndi ndani? Abweretu kuti tilimbane! Ambuye Yehova ndiye amene amandithandiza. Ndaninso amene adzanditsutsa? Onse adzatha ngati chovala chodyedwa ndi njenjete.
“Odala ndi amene zoyipa zawo zakhululukidwa; amene machimo awo afafanizidwa. Ngodala munthu amene machimo ake Ambuye sadzawakumbukiranso.”
Tsopano popeza tayesedwa olungama mwa chikhulupiriro, tili ndi mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
ndipo onse alungamitsidwa mwaulere mwa chisomo chake chifukwa cha Khristu Yesu amene anawawombola.
“Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene amamva mawu anga ndi kukhulupirira Iye amene ananditumiza Ine, ali ndi moyo wosatha ndipo sadzaweruzidwa. Iye wachoka mu imfa ndipo walowa mʼmoyo.
Pamene munali akufa chifukwa cha machimo anu ndi osachita mdulidwe mʼmitima mwanu, Mulungu anakupatsani moyo mwa Khristu. Iye anatikhululukira machimo athu onse. Anafafaniza kalata ya ngongole yathu, pomwe panali milandu yotitsutsa ife. Iye anayichotsa, nayikhomera pa mtanda.
Popeza chifukwa cha magazi ake ife tapezeka olungama pamaso pa Mulungu, Iyeyo adzatipulumutsa koposa kotani ku mkwiyo wa Mulungu.