Mavesi a m'Baibulo Onena za Owerengedwa Olungama

Mavesi 12 a m'Baibulo onena za Owerengedwa Olungama oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Aroma 4:5

Koma kwa munthu amene sanagwire ntchito ndipo akhulupirira Mulungu amene amalungamitsa ochimwa, chikhulupiriro chakecho chimatengedwa kukhala chilungamo.

02 Aroma 4:3

Kodi Malemba akuti chiyani? “Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo ichi chinamuchititsa kukhala wolungama.”

03 Genesis 15:6

Abramu anakhulupirira Yehova, ndipo ichi chinamuchititsa kukhala wolungama.

04 Agalatiya 3:6

Nʼchimodzimodzinso Abrahamu, “Iye anakhulupirira Mulungu, ndipo Mulungu anamutenga kukhala wolungama.”

05 Aroma 4:22-24

Nʼchifukwa chake “chinamuchititsa kukhala wolungama.” Mawu akuti, “chinatengedwa kwa iye” sanalembedwe chifukwa cha iye yekha, komanso chifukwa ife amene Mulungu adzatiyesa olungama, ife amene tikhulupirira mwa Iye amene anamuukitsa kwa akufa, Yesu Ambuye athu.

06 Aroma 4:9

Kodi madalitso amenewa ali kwa ochita mdulidwe okha kapena kwa amene sanachitepo mdulidwe? Ife takhala tikunena kuti chikhulupiriro cha Abrahamu chinamuchititsa kukhala wolungama.

07 Aroma 4:6

Davide ponena zomwezi pamene anayankhula za kudala kwa munthu amene Mulungu amulungamitsa osati chifukwa cha ntchito zake akuti,

08 Masalimo 32:2

Ngodala munthu amene machimo ake Yehova sawawerengeranso pa iye ndipo mu mzimu mwake mulibe chinyengo.

09 Yakobo 2:23

Ndipo Malemba akunena kuti, “Abrahamu anakhulupirira Mulungu ndipo anatengedwa kukhala wolungama,” ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu.

10 Aroma 4:11

Ndipo iye anachita mdulidwe ngati chizindikiro ndi chitsimikizo cha kulungama kumene anali nako mwachikhulupiriro pomwe anali asanachite mdulidwe. Choncho, iye ndi kholo la onse amene akhulupirira koma sanachite mdulidwe, ndi cholinga chakuti alungamitsidwe.

11 Afilipi 3:9

ndi kuti ndipezeke mwa Iyeyo, osati ndi chilungamo changa chobwera chifukwa chotsata malamulo, koma chimene chimabwera chifukwa chokhulupirira Khristu. Chilungamochi nʼchochokera kwa Mulungu, timachilandira mwachikhulupiriro.

12 2 Akorinto 5:21

Chifukwa cha ife, Mulungu anasandutsa wopanda tchimoyo kukhala tchimo, kuti mwa Iye ife tikakhale chilungamo cha Mulungu.

Mitu yofanana