Mavesi a m'Baibulo Onena za Chilungamo cha Mulungu

Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Chilungamo cha Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Afilipi 3:9

ndi kuti ndipezeke mwa Iyeyo, osati ndi chilungamo changa chobwera chifukwa chotsata malamulo, koma chimene chimabwera chifukwa chokhulupirira Khristu. Chilungamochi nʼchochokera kwa Mulungu, timachilandira mwachikhulupiriro.

02 2 Akorinto 5:21

Chifukwa cha ife, Mulungu anasandutsa wopanda tchimoyo kukhala tchimo, kuti mwa Iye ife tikakhale chilungamo cha Mulungu.

03 Aroma 3:21-22

Koma tsopano chilungamo chochokera kwa Mulungu, osati chochokera ku Malamulo, chaonetsedwa. Ichi ndi chimene Malamulo ndi Aneneri amachitira umboni. Timakhala olungama pamaso pa Mulungu pamene takhulupirira Yesu Khristu. Mulungu amachitira zimenezi anthu onse amene akhulupirira Khristu. Palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi a mitundu ina,

04 Aroma 1:17

Pakuti mu Uthenga Wabwino anawulula kuti chilungamo chimachokera kwa Mulungu. Kuyambira pachiyambi mpaka potsiriza ndi chilungamo chobwera mwachikhulupiriro, monga kwalembedwera kuti, “Wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.”

05 Yeremiya 23:6

Pa masiku a ulamuliro wake Yuda adzapulumuka ndipo Israeli adzakhala pamtendere. Dzina limene adzamutcha ndi ili: Yehova ndiye Chilungamo Chathu.

06 Aroma 3:26

Iye anachita izi kuti aonetse chilungamo chake lero lino. Anthu azindikire kuti Iye ndi wolungama ndipo amalungamitsa aliyense amene akhulupirira Yesu.

07 Aroma 10:3-4

Pakuti sanadziwe chilungamo chochokera kwa Mulungu ndipo anafuna kukhazikitsa chawochawo. Iwo sanagonjere chilungamo cha Mulungu. Khristu ndiye mathero amalamulo kuti aliyense amene akhulupirira akhale olungama pamaso pa Mulungu.

08 Yesaya 61:10

Ine ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Yehova; moyo wanga ukukondwera chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso, ndipo wandiveka mkanjo wachilungamo. Zili ngati mkwati wovala nkhata ya maluwa mʼkhosi mwake, ndiponso ngati mkwatibwi wovala mikanda yamtengowapatali.

Mitu yofanana