Mavesi a m'Baibulo Onena za Ana a Mulungu

Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Ana a Mulungu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Yohane 1:12

Koma kwa onse amene anamulandira Iye, kwa amene anakhulupirira mʼdzina lake, Iye anawapatsa mphamvu yokhala ana a Mulungu;

02 1 Yohane 3:1

Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye.

03 Aroma 8:16

Mzimu mwini amavomerezana ndi mzimu wathu kuti ife ndife ana a Mulungu.

04 Agalatiya 3:26

Nonse ndinu ana a Mulungu kudzera mʼchikhulupiriro mwa Khristu Yesu,

05 Aroma 8:14

Onse amene amatsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu ndi ana a Mulungu.

06 1 Yohane 3:2

Abale okondedwa, tsopano ndife ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Koma tikudziwa kuti Yesu akadzaonekera, tidzafanana naye, pakuti tidzamuona Iyeyo monga momwe alili.

07 Afilipi 2:15

kuti mukhale wopanda cholakwa ndi angwiro, ana a Mulungu wopanda cholakwika mu mʼbado uno wachinyengo ndi wosocheretsa. Mukatero mudzawala pakati pawo ngati nyenyezi zakumwamba

08 Yohane 11:52

ndipo osati mtundu okhawo komanso kwa ana ena a Mulungu onse obalalikana, kuti awabweretse pamodzi ndi kuwapanga kukhala amodzi.

Mitu yofanana