Mavesi a m'Baibulo Onena za Kutengedwa Kukhala Ana
Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Kutengedwa Kukhala Ana oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
kudzawombola amene anali pansi pa lamulo, kuti tilandiridwe monga ana.
Mzimu amene inu munalandira samakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha, koma Mzimu amakusandutsani ana. Ndipo mwa Iye ife timafuwula kuti, “Abba, Atate.”
Iye anakonzeratu kuti ife titengedwe ngati ana mwa Yesu Khristu, molingana ndi kukonda kwake ndi chifuniro chake.
Koma kwa onse amene anamulandira Iye, kwa amene anakhulupirira mʼdzina lake, Iye anawapatsa mphamvu yokhala ana a Mulungu;
Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye.
Nonse ndinu ana a Mulungu kudzera mʼchikhulupiriro mwa Khristu Yesu,
Anachita zimenezi kuti tiziyamika ulemerero wa chisomo chake, umene watipatsa kwaulere mwa Khristu amene amamukonda.
Si zokhazo ayi, ngakhale ife tomwe, amene tili ndi zipatso zoyamba za Mzimu, tikubuwulira mʼkati mwathu pomwe tikudikira mwachidwi kusankhidwa kwathu ngati ana, kuwomboledwa kwa matupi athu.
Ndipo “Ndidzakhala Atate anu, ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi, akutero Ambuye, Wamphamvuzonse.”