Mavesi a m'Baibulo Onena za Olowa Nyumba Pamodzi ndi Khristu

Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Olowa Nyumba Pamodzi ndi Khristu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Aroma 8:17

Tsono ngati tili ana ake, ndiye kuti ndife olowa mʼmalo a Mulungu ndi olowa mʼmalo pamodzi ndi Khristu. Ngati ife timva zowawa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.

02 Agalatiya 4:7

Choncho sindiwenso kapolo, koma mwana wa Mulungu. Tsono popeza ndiwe mwana wake, Mulungu wakusandutsanso mlowamʼmalo.

03 Tito 3:7

kuti titalungamitsidwa mwachisomo chake, tikhale olowamʼmalo okhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha.

04 Aroma 8:16-17

Mzimu mwini amavomerezana ndi mzimu wathu kuti ife ndife ana a Mulungu. Tsono ngati tili ana ake, ndiye kuti ndife olowa mʼmalo a Mulungu ndi olowa mʼmalo pamodzi ndi Khristu. Ngati ife timva zowawa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.

05 Aefeso 1:11

Iye anatisankhiratu mwa Khristu, atatikonzeratu molingana ndi machitidwe a Iye amene amachititsa zinthu zonse kuti zikwaniritse cholinga cha chifuniro chake,

06 Agalatiya 3:29

Ngati inu muli ake a Khristu, ndiye kuti ndinu mbewu ya Abrahamu, ndi olowamʼmalo molingana ndi lonjezo.

07 1 Petro 1:4

kuti tidzalandire chuma chomwe sichingawonongeke, kuyipitsidwa kapena kufota. Chuma chimenechi akukusungirani kumwamba.

08 Akolose 1:12

ndi kuyamika Atate nthawi zonse, amene wakuyenerezani kuti mulandire nawo chuma cha oyera mtima mu ufumu wa kuwunika.

09 Aefeso 1:14

Mzimu Woyerayo ndi chikole chotsimikizira kuti tidzalandira madalitso athu, ndipo kuti Mulungu anatiwombola kuti tikhale anthu ake. Iye anachita zimenezi kuti timuyamike ndi kumulemekeza.

10 Agalatiya 4:1-2

Chimene ndikunena ndi chakuti, ngati mlowamʼmalo akali wamngʼono, sasiyana ndi kapolo, ngakhale kuti chuma chonse ndi chake. Mwanayo ayenera kumvera omulera ndiponso anthu oyangʼanira chuma mpaka nthawi imene abambo ake anakhazikitsa.

11 Aroma 8:32

Iye amene sanatimane Mwana wake wa Iye yekha, koma anamupereka chifukwa cha ife tonse. Iye adzalekeranjinso pamodzi naye kutipatsa ife zinthu zonse mwaulere?

12 Ahebri 9:15

Pa chifukwa chimenechi Khristu ndi mʼkhalapakati wa pangano latsopano, kuti iwo amene anayitanidwa alandire chuma chamuyaya, pakuti Iye tsopano anafa ngati dipo lomasula iwo ku machimo amene anachita ali pansi pa pangano loyamba lija.

13 Yakobo 2:5

Tamverani abale anga okondedwa, kodi Mulungu sanasankhe amene dziko lapansi limawaona ngati amphawi kuti akhale olemera mʼchikhulupiriro ndi kulowa ufumu umene Iye analonjeza kwa amene amamukonda?

14 Aefeso 3:6

Chinsinsicho nʼchakuti, kudzera mu Uthenga Wabwino anthu a mitundu ina ndi olowamʼmalo pamodzi ndi Aisraeli, ndi ziwalo za thupi limodzi, ndi olandira nawo pamodzi malonjezo a mwa Khristu Yesu.

Mitu yofanana