Mavesi a m'Baibulo Onena za Lero Ndilo Tsiku

Mavesi 5 a m'Baibulo onena za Lero Ndilo Tsiku oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 2 Akorinto 6:2

Pakuti akunena kuti, “Pa nthawi yanga yabwino yokomera anthu mtima ndinakumvera, ndipo pa nthawi yopulumutsa ndinakuthandiza. Taonani, ndikukuwuzani kuti, ino ndiyo nthawi yabwino ya Ambuye, lero ndiye tsiku la chipulumutso.”

02 Ahebri 3:15

Monga kunanenedwa kuti, “Lero ngati mumva mawu ake, musawumitse mitima yanu ngati momwe munachitira pamene munawukira.”

03 Ahebri 4:7

Nʼchifukwa chake Mulungu anayikanso tsiku lina limene analitcha “Lero.” Patapita nthawi yayitali Iye anayankhula za tsiku lomweli kudzera mwa Davide, monga ndinanena kale kuti, “Lero mukamva mawu ake, musawumitse mitima yanu.”

04 Yesaya 55:6

Funafunani Yehova pamene Iye akupezeka. Mupemphere kwa Iye pamene ali pafupi.

05 2 Akorinto 5:20

Choncho ife ndi akazembe a Khristu, monga ngati Mulungu akudandaulira anthu kudzera mwa ife. Ife tikukupemphani inu mʼmalo mwa Khristu kuti, yanjanitsidwani ndi Mulungu.

Mitu yofanana