Mavesi a m'Baibulo Onena za Kufatsa
Mavesi 6 a m'Baibulo onena za Kufatsa oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Odala ndi amene ali ofatsa, chifukwa adzalandira dziko lapansi.
kufatsa ndi kudziretsa. Palibe lamulo loletsa zimenezi.
(Koma Mose anali munthu wodzichepetsa kwambiri kuposa munthu aliyense pa dziko lapansi).
Mʼmalo mwake kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa munthu wa mʼkatimo, kukongola kosatha kwa mtima ofatsa ndi mzimu wachete, zimene ndi za mtengowapatali pamaso pa Mulungu.
Funafunani Yehova, inu nonse odzichepetsa a mʼdziko, inu amene mumachita zimene amakulamulani. Funafunani chilungamo, funafunani kudzichepetsa; mwina mudzatetezedwa pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.
Choncho, ngati anthu osankhidwa ndi Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa kwambiri, muvale chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa ndi kupirira.