Mavesi a m'Baibulo Onena za Kwezani Manja Anu
Mavesi 14 a m'Baibulo onena za Kwezani Manja Anu oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
Kwezani manja anu mʼmalo opatulika ndipo mutamande Yehova.
Ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga, ndipo mʼdzina lanu ndidzakweza manja anga.
Choncho ndikufuna kuti paliponse popemphera, amuna azikweza manja awo kwa Mulungu mopanda mkwiyo kapena kukangana.
Pemphero langa lifike kwa Inu ngati lubani; kukweza manja kwanga kukhale ngati nsembe yamadzulo.
Tiyeni tikweze mitima yathu ndi manja athu kwa Mulungu kumwamba ndipo tinene kuti:
Imvani kupempha chifundo kwanga pomwe ndikuyitana kwa Inu kuti mundithandize, pomwe ndikukweza manja anga kuloza ku malo anu oyeretsetsa.
Ezara anatamanda Yehova, Mulungu wamkulu, ndipo anthu onse anakweza manja awo ndi kuyankha kuti, “Ameni, ameni.” Pambuyo pake onse anaweramitsa pansi mitu yawo napembedza Yehova akanali chizolikire choncho.
maso anga ada ndi chisoni. Ndimayitana Inu Yehova tsiku lililonse; ndimakweza manja anga kwa Inu.
Ndikweza manja anga ku malamulo anu, ku malamulo amene ndimawakonda, ndipo ndimalingalira malangizo anu.
Ndatambalitsa manja anga kwa Inu; moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu monga nthaka yowuma. Sela
Mose ankati akakweza manja ake, Aisraeli amapambana, koma akatsitsa manja akewo Amaleki amapambana.
Ombani mʼmanja, inu anthu onse; fuwulani kwa Mulungu ndi mawu achimwemwe.
mapiri anakuonani ndipo anagwedezeka. Madzi amphamvu anasefukira; nyanja yozama inakokoma ndipo mafunde ake anakwera kwambiri.
Pamenepo Solomoni anayimirira patsogolo pa guwa lansembe la Yehova pamaso pa gulu lonse la Aisraeli ndipo anakweza manja ake kumwamba,