Mavesi a m'Baibulo Onena za Oyesedwa Olungama Mwaulere

Mavesi 8 a m'Baibulo onena za Oyesedwa Olungama Mwaulere oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Aroma 3:24

ndipo onse alungamitsidwa mwaulere mwa chisomo chake chifukwa cha Khristu Yesu amene anawawombola.

02 Aroma 5:1

Tsopano popeza tayesedwa olungama mwa chikhulupiriro, tili ndi mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.

03 Aroma 3:28

Ife tikunenabe kuti munthu amalungamitsidwa mwachikhulupiriro osati mwakusunga Malamulo.

04 Agalatiya 2:16

tikudziwa kuti munthu salungamitsidwa pochita ntchito za lamulo koma ndi chikhulupiriro mwa Yesu Khristu. Chomwecho, ifenso tinakhulupirira Khristu Yesu kuti tilungamitsidwe mwachikhulupiriro mwa Khristu ndipo osati pochita ntchito za lamulo, chifukwa palibe amene adzalungamitsidwa pochita ntchito za lamulo.

05 Tito 3:7

kuti titalungamitsidwa mwachisomo chake, tikhale olowamʼmalo okhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha.

06 Aroma 4:25

Iye anaperekedwa kuti aphedwe chifukwa cha machimo athu ndipo anaukitsidwa ndi kukhala ndi moyo kuti tilungamitsidwe.

07 Aroma 8:30

Iwo amene anawasankhiratu, anawayitananso. Amene Iye anawayitana anawalungamitsanso ndipo amene anawalungamitsa anawapatsanso ulemerero.

08 1 Akorinto 6:11

Ndipo umu ndi mmene ena mwa inu munalili. Koma munatsukidwa, munayeretsedwa, munalungamitsidwa mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu ndi Mzimu wa Mulungu wathu.

Mitu yofanana