Mavesi a m'Baibulo Onena za Uthenga Wabwino kwa Osauka
Mavesi 11 a m'Baibulo onena za Uthenga Wabwino kwa Osauka oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.
“Mzimu wa Ambuye ali pa Ine; chifukwa wandidzoza kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kwa osauka. Wandituma kuti ndilalikire kwa a mʼndende kuti amasulidwe ndi kwa osaona kuti apenyenso, kumasulidwa kwa osautsidwa,
Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine, chifukwa Yehova wandidzoza kuti ndilalikire uthenga wabwino kwa anthu osauka. Wandituma kuti ndikatonthoze anthu osweka mtima, ndikalengeze kwa akapolo kuti alandire ufulu ndiponso kuti ndikamasule a mʼndende.
Osaona akuona, olumala akuyenda, akhate akuchiritsidwa, osamva akumva, akufa akuukitsidwa ndipo Uthenga Wabwino ukulalikidwa kwa osauka.
Akuyangʼana ophunzira ake, Iye anati, “Odala ndinu amene ndi osauka, chifukwa ufumu wa Mulungu ndi wanu.
Tamverani abale anga okondedwa, kodi Mulungu sanasankhe amene dziko lapansi limawaona ngati amphawi kuti akhale olemera mʼchikhulupiriro ndi kulowa ufumu umene Iye analonjeza kwa amene amamukonda?
Munthu wosauka uno anayitana, ndipo Yehova anamumva; Yehova anamupulumutsa ku mavuto ake onse.
Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine, chifukwa Yehova wandidzoza kuti ndilalikire uthenga wabwino kwa anthu osauka. Wandituma kuti ndikatonthoze anthu osweka mtima, ndikalengeze kwa akapolo kuti alandire ufulu ndiponso kuti ndikamasule a mʼndende. Wandituma kuti ndikalengeze nthawi imene Yehova adzapulumutsa anthu ake; za tsiku limene Yehova adzalanga adani a anthu ake. Wandituma kuti ndikatonthoze olira.
Koma osowa sadzayiwalika nthawi zonse, kapena chiyembekezo cha ozunzika kutayika nthawi zonse.
Iye wakhutitsa a njala ndi zinthu zabwino koma anachotsa olemera wopanda kanthu.
Iye amakweza munthu wosauka kuchoka pa fumbi ndi kutukula munthu wosowa kuchoka pa dzala;
Iye amakweza osauka kuwachotsa pa fumbi, ndipo amachotsa anthu osowa pa dzala. Iye amawakhazika pamodzi ndi ana a mafumu, amawapatsa mpando waulemu. “Pakuti nsanamira za dziko lapansi ndi za Yehova, anakhazika dziko lapansi pa nsanamirazo.