Mavesi a m'Baibulo Onena za Chisomo ndi Ntchito

Mavesi 9 a m'Baibulo onena za Chisomo ndi Ntchito oti muwerenge, musinkhasinkhe, ndi kuloweza.

01 Aefeso 2:9

osati ndi ntchito, kuti wina aliyense asadzitamandire.

02 Aefeso 2:8-9

Pakuti mwapulumutsidwa mwachisomo, kudzera mʼchikhulupiriro ndipo izi sizochokera mwa inu eni, koma ndi mphatso ya Mulungu, osati ndi ntchito, kuti wina aliyense asadzitamandire.

03 Agalatiya 2:16

tikudziwa kuti munthu salungamitsidwa pochita ntchito za lamulo koma ndi chikhulupiriro mwa Yesu Khristu. Chomwecho, ifenso tinakhulupirira Khristu Yesu kuti tilungamitsidwe mwachikhulupiriro mwa Khristu ndipo osati pochita ntchito za lamulo, chifukwa palibe amene adzalungamitsidwa pochita ntchito za lamulo.

04 Aroma 4:5

Koma kwa munthu amene sanagwire ntchito ndipo akhulupirira Mulungu amene amalungamitsa ochimwa, chikhulupiriro chakecho chimatengedwa kukhala chilungamo.

05 Tito 3:5

Iye anatipulumutsa, osati chifukwa cha ntchito zathu zolungama zimene tinachita koma chifukwa cha chifundo chake. Anatipulumutsa potisambitsa, kutibadwitsa kwatsopano ndi kutikonzanso mwa Mzimu Woyera

06 Agalatiya 3:11

Chodziwikiratu nʼchakuti palibe amene amalungamitsidwa pamaso pa Mulungu ndi lamulo, chifukwa, “Wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.”

07 Aroma 4:4

Tsopano munthu amene wagwira ntchito, malipiro ake satengedwa kukhala ngati mphatso koma zimene anayenera kulandira.

08 Aroma 11:6

Ndipo ngati ndi mwachisomo, sikungakhalenso mwa ntchito. Ngati zikanatero, chisomo sichikanakhalanso chisomo ayi.

09 Afilipi 3:9

ndi kuti ndipezeke mwa Iyeyo, osati ndi chilungamo changa chobwera chifukwa chotsata malamulo, koma chimene chimabwera chifukwa chokhulupirira Khristu. Chilungamochi nʼchochokera kwa Mulungu, timachilandira mwachikhulupiriro.

Mitu yofanana